Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. |
| 2 |
| Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), |
| 3 |
| kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko. |
| 4 |
| Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye. |
| 5 |
| Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukira kanthu kena, monga kwa Khristu; |
| 6 |
| si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima; |
| 7 |
| akuchita ukapolo ndi kuvomereza mtima, monga kutumikira Ambuye Yesu Khristu, si anthu ai; |
| 8 |
| podziwa kuti chinthu chokoma chilichonse yense achichita, adzambwezera chomwechi Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu. |
| 9 |
| Ndipo, ambuye, inu, muwachitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali m'Mwamba, ndipo palibe tsankho kwa Iye. |
| 10 |
| Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. |
| 11 |
| Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. |
| 12 |
| Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba. |
| 13 |
| Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika. |
| 14 |
| Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo; |
| 15 |
| ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere; |
| 16 |
| koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. |
| 17 |
| Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu; |
| 18 |
| mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse, |
| 19 |
| ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino, |
| 20 |
| chifukwa cha umene ndili mtumiki wa m'unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula. |
| 21 |
| Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; |
| 22 |
| amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. |
| 23 |
| Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. |
| 24 |
| Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/ephesians/006.mp3
6
6