Mutalanda maiko a anthuwo, musadzalephere kuwononga kwathunthu malo onse amene iwo amapembedzerapo milungu yao, monga pa mapiri aatali ndi pa mapiri aafupi, ndiponso pansi pa mitengo yogudira.
Mukagwetse maguwa ao, ndipo miyala yao yoimiritsa, imene amaiyesa yopembedzerapo, mukaiphwanyephwanye. Mukatenthe mafano ao a Aserimu. Mukaonongenso mafano ao ofanizira milungu yao, ndipo mukafafanize ndi dzina lomwe la milunguyo konsekonse.
Muzikapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zanu zina, zopereka zanu zachikhumi, ndi zopereka za mtundu wina, ndiponso mphatso zimene mumalonjeza kupereka kwa Mulungu, zopereka zanu zaufulu, ndiponso ana oyamba kubadwa a ng'ombe ndi a zoŵeta zina.
Kumenekonso inu pamodzi ndi mabanja anu mudzadya ndi kusangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, chifukwa cha madalitso amene Iyeyo adatsitsa pa inu, kuti ntchito zanu zonse ziyende bwino.
Tsono mudzakondwa pamaso pake inuyo, ana anu aamuna ndi aakazi, antchito anu aamuna ndi aakazi, pamodzi ndi Alevi amene ali m'midzi mwanu, poti paja iwo sadzalandira dziko laolao.
Ku midzi yonse kumene mukakhale, musadzadye chachikhumi cha tirigu wanu, kapena cha vinyo wanu kapena cha mafuta anu aolivi. Kumenekonso musakadye kalikonse kamene mwakapereka kwa Chauta, monga ana a ng'ombe ndi a zoŵeta zina oyamba kubadwa, kapena mphatso zimene mwalonjeza kuti mudzapereka kwa Chauta, kapena zopereka zanu zaufulu, kapena zopereka zina zilizonse.
Inuyo ndi ana anu, pamodzi ndi antchito anu, ndi Alevi amene akhala m'midzi mwanu, muzikadya zopereka zonsezi pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, pa malo amodzi amene Chauta, Mulungu wanu, adzakhala atasankha. Kumenekonso muzidzasangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, chifukwa cha ntchito zanu zonse zoyenda bwino.
Kumeneko mukapereke nsembe zopsereza, nyama ndi magazi omwe, pa guwa la Chauta. Magazi ake mukathire pa guwa la Chauta, Mulungu wanu, koma nyama yake mungathe kudya.
Musadzapembedze Chauta, Mulungu wanu, mofanafana ndi m'mene iwo amapembedzera milungu yaoyo. Iwo adachita zoipa zoopsa zambiri zimene Chauta amadana nazo, mpaka kutentha ana ao aamuna ndi aakazi pa moto pakuŵapereka kwa milungu yao.