Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ansembe Alevi, fuko lonse la Levi, alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi Israele; azizidya nsembe zamoto za Yehova, ndi cholowa chake. |
| 2 |
| Alibe cholowa pakati pa abale ao; Yehova mwini wake ndiye cholowa chao, monga ananena nao. |
| 3 |
| Ndipo zoyenera ansembe, awapatse anthu akuphera nsembe ndizo: ingakhale ng'ombe kapena nkhosa azipatsa wansembe mwendo wamwamba, ndi ya m'masaya ndi chifu. |
| 4 |
| Zipatso zoyamba za tirigu wanu, za vinyo wanu, ndi za mafuta anu ndi ubweya woyamba kuusenga, muwapatse izi. |
| 5 |
| Popeza Yehova Mulungu wanu anawasankha mwa mafuko anu onse, aimirire natumikire m'dzina la Yehova, iwo ndi ana ao amuna kosalekeza. |
| 6 |
| Ndipo Mlevi akachokera kumudzi wanu wina m'Israele monse, kumene akhalako, nakadza ndi chifuniro chonse cha moyo wake ku malo amene Yehova adzasankha; |
| 7 |
| pamenepo azitumikira m'dzina la Yehova Mulungu wake, monga amachita abale ake onse Alevi akuimirirako pamaso pa Yehova. |
| 8 |
| Chakudya chao chizifanana, osawerengapo zolowa zake zogulitsa. |
| 9 |
| Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musamaphunzira kuchita monga mwa zonyansa za amitundu aja. |
| 10 |
| Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. |
| 11 |
| Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. |
| 12 |
| Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu. |
| 13 |
| Mukhale angwiro ndi Yehova Mulungu wanu. |
| 14 |
| Pakuti amitundu awa amene mudzawalandira, amamvera iwo akuyesa mitambo, ndi a ula; koma inu, Yehova Mulungu wanu sakulolani kuchita chotero. |
| 15 |
| Yehova Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri wa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye; |
| 16 |
| monga mwa zonse munafunsa Yehova Mulungu wanu m'Horebu, tsiku lakusonkhana lija, ndi kuti, Tisamvenso mau a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso moto waukulu uwu, kuti tingafe. |
| 17 |
| Ndipo Yehova anati kwa ine, Chokoma ananenachi. |
| 18 |
| Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale ao, wonga iwe; ndipo ndidzampatsa mau anga m'kamwa mwake, ndipo adzanena nao zonse ndimuuzazi. |
| 19 |
| Ndipo kudzakhala kuti munthu wosamvera mau anga amene amanena m'dzina langa, ndidzamfunsa. |
| 20 |
| Koma mneneri wakuchita modzikuza ndi kunena mau m'dzina langa, amene sindinamlamulira anene, kapena kunena m'dzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe. |
| 21 |
| Ndipo mukati m'mtima mwanu, Tidzazindikira bwanji mau amene Yehova sananene? |
| 22 |
| Mneneri akanena m'dzina la Yehova, koma mau adanenawa sachitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanene; mneneriyo ananena modzikuza, musamuope iye. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/deuteronomy/018.mp3
34
18