Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Pamenepo tinabwerera, ndi kuyenda kumka kucipululu, kutsata njira ya Nyanja Yofiira, monga Yehova adanena ndi ine; ndipo tinapaza phiri la Seiri masiku ambiri. |
| 2 |
| Ndipo Yehova ananena ndi ine, ndi kuti, |
| 3 |
| Yakwanira nthawi yakupaza inu phiri ili; tembenukani kumka kumpoto, |
| 4 |
| Ndipo uuze anthu, ndi kuti, Mukapite kubzyola malire a abale anu, ana a Bsau okhala m'Seiri; ndipo adzakuopani; mucenjere ndithu; |
| 5 |
| musalimbana nao; popeza sindikupatsakoni dziko lao, pangakhale popondapo phazi lanu ai pakuti ndapatsa Bsau phiri la Seiri likhale lace lace. |
| 6 |
| Mugulane nao cakudya ndi ndarama, kuti mudye; mugulane naonso madzi kuti mumwe. |
| 7 |
| Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu nchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m'cipululu ici cacikuru; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowa kanthu. |
| 8 |
| Potero tinapitirira abale athu, ana a Bsau okhala m'Seiri, njira ya cidikha, ku Elati ndi ku Ezioni Geberi. |
| 9 |
| Pamenepo tinatembenuka ndi kudzera njira ya cipululu ca Moabu. Ndipo Yehova anati kwa ine, Usabvuta Moabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lace likhale lako lako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale lao lao. |
| 10 |
| (Aemi anakhalamo kale, ndiwo anthu akuru, ndi ambiri, ndi atalitali, ngati Aanaki. |
| 11 |
| Anawayesa iwonso Arefai, monga Aanaki; koma Amoabu awacha Aemi. |
| 12 |
| Ndipo Ahori anakhala m'Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m'malo mwao; monga Israyeli anacitira dziko lace lace, limene Yehova anampatsa.) |
| 13 |
| Ukani tsopano, olokani mtsinje wa Zeredi. Ndipo tinaoloka mtsinje wa Zeredi. |
| 14 |
| Ndipo masiku amene tinayenda kucokera ku Kadesi Barinea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'cigono, monga Yehova adawalumbirira. |
| 15 |
| Komanso dzanja la Yehova linatsutsana nao, kuwaononga m'cigono, kufikira adawatha. |
| 16 |
| Ndipo kunali, atatha kufa amuna onse ankhondo mwa anthu, |
| 17 |
| Yehova ananena ndi ine, ndi kuti, |
| 18 |
| Lero lomwe utumphe malire a Moabu, ndiwo Ari. |
| 19 |
| Ndipo pamene uyandikiza popenyana ndi ana a Amoni, usawabvuta, kapena kuutsana nao; popeza sindidzakupatsako dziko la ana a Amoni likhale lako lako; popeza ndinapatsa ana a Loti ili likhale lao lao. |
| 20 |
| (Ilinso aliyesa dziko la Arefai; Arefai anakhalamo kale; koma Aamoni awacha Azamzumi; |
| 21 |
| ndiwo anthu akuru, ndi ambiri, ndi atalitali, monga Aanaki; koma Yehova anawaononga pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao; |
| 22 |
| monga iye anacitira ana a Bsau, akukhala m'Seiri, pamene anaononga Ahori pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao kufikira lero lomwe. |
| 23 |
| Kunena za Aavi akukhala m'midzi kufikira ku Gaza, Akafitori, akufuma ku Kafitori, anawaononga, nakhala m'malo mwao.) |
| 24 |
| Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, M-amori, ndi dziko lace m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo. |
| 25 |
| Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kucititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa cifukwa ca iwe. |
| 26 |
| Ndipo ndinatuma amithenga ocokera ku cipululu ca Kedemoti kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi mau a mtendere, ndi kuti, |
| 27 |
| Ndipitire m'dziko mwako; ndidzatsata mseu, osapatuka ine ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, |
| 28 |
| Undigulitse cakudya ndi ndarama, kuti ndidye; ndi kundipatsa madzi kwa ndarama, kuti ndimwe; cokhaci ndipitire coyenda pansi; |
| 29 |
| monga anandicitira ana a Esau akukhala m'Seiri, ndi Amoabu akukhala m'Ari; kufikira nditaoloka Yordano kulowa dziko limene Yehova Mulungu wathu atipatsa. |
| 30 |
| Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilola kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wace, nalimbitsa mtima wace, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino. |
| 31 |
| Ndipo Yehova anati kwa ine, Taona, ndayamba kupereka Sihoni ndi dziko lace pamaso pako; yamba kulandira dziko lace likhale lako lako. |
| 32 |
| Pamenepo Sihoni anaturuka kukomana nafe, iye ndi anthu ace onse, kugwirana nafe nkhondo ku Yahaza. |
| 33 |
| Ndipo Yehova Mulungu wathu anampereka iye pamaso pathu; ndipo tinamkantha, iye ndi ana ace amuna ndi anthu ace onse. |
| 34 |
| Ndipo muja tinalanda midzi yace yonse; ndipo tinaononga konse midzi yonse, amuna ndi akazi ndi ana; sitinasiyapo ndi mmodzi yense. |
| 35 |
| Zoweta zokha tinadzifunkhira, pamodzi ndi zofunkha za midzi tidailanda. |
| 36 |
| Kuyambira ku Aroeri, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi ku mudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Gileadi, kunalibe mudzi wakutitalikira malinga ace; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu. |
| 37 |
| Ku dziko la ana a Amoni lokha simunayandikiza; dera lonse la mtsinje wa Yaboki, ndi midzi ya kumapiri, ndi kwina kuli konse Yehova Mulungu wathu anatiletsa. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/deuteronomy/002.mp3
34
2