Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Pamene muturuka pa mdani wanu kunkhondo, ndi kuona akavalo ndi magareta ndi anthu akucurukira inu, musawaopa; popeza Yehova Mulungu wanu, amene anakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto, ali ndi inu. |
| 2 |
| Ndipo kudzali, pamene muyandikiza kunkhondo, ayandikize wansembe nanene ndi anthu, |
| 3 |
| nati nao, Tamverani, Israyeli, muyandikiza kunkhondo lero paadani anu; musalumuka mitima yanu; musacita mantha, kapena kunjenjemera, kapena kuopsedwa pamaso pao; |
| 4 |
| pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye wakumuka nanu, kugwirira inu pa adani anu, kukupulumutsani. |
| 5 |
| Ndipo akapitao anene ndi anthu, ndi kuti, Ndani munthuyo anamanga nyumba yatsopano, osalowamo? amuke nabwerere kunyumba kwace, kuti angafe kunkhondo nangalowemo munthu wina. |
| 6 |
| Ndipo ndani munthuyo ananka munda wamphesa osalawa zipatso zace? amuke nabwerere ku nyumba yace, kuti angafe kunkhondo, nangalawe munthu wina zipatso zace. |
| 7 |
| Ndipo munthuyo ndani anapala bwenzi ndi mkazi osamtenga? amuke nabwerere kunyumba kwace, kuti angafe kunkhondo, nangamtenge munthu wina. |
| 8 |
| Pamenepo akapitao anenenso kwa anthu, ndi kuti, Munthuyo ndani wakucita mantha ndi wofumuka mtima? amuke nabwerere kunyumba kwace, ingasungunuke mitima ya abale ace monga mtima wace. |
| 9 |
| Ndipo kudzali, atatha akapitao kunena ndi anthu, aike akazembe a makamu atsogolere anthu. |
| 10 |
| Pamene muyandikiza mudzi kucita nao nkhondo, muziupfuulira ndi mtendere. |
| 11 |
| Ndipo kudzali, ukakubwezerani mau a mtendere, ndi kukutsegulirani, pamenepo anthu onse opereka m'mwemo akhale alambi anu, nadzakutumikirani. |
| 12 |
| Koma ukapanda kucita zamtendere ndi inu, koma kucita nkhondo nanu, pamenepo uumangire tsasa. |
| 13 |
| Ndipo pamene Yehova Mulungu wanu aupereka m'dzanja lanu, mukanthe amuna ace onse ndi lupanga lakuthwa. |
| 14 |
| Koma akazi ndi ana ndi ng'ombe ndi zonse ziti m'mudzimo, zankhondo zace zonse, mudzifunkhire nokha; ndipo mudye zankhondo za adani anu, zimene Yehova Mulungu wanu anakupatsani. |
| 15 |
| Muzitero nayo midzi yonse yokhala kutaritari ndi inu, yosakhala midzi ya amitundu awa. |
| 16 |
| Koma za midzi ya amitundu awa, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ikhale colowa canu, musasiyepo camoyo ciri conse cakupuma; |
| 17 |
| koma muwaononge konse Ahiti, ndi Aamori, Akanani, ndi Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi; monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani; |
| 18 |
| kuti angakuphunzitseni kucita monga mwa zonyansa zao zonse, amazicitira milungu yao; ndipo mungacimwire Yehova Mulungu wanu. |
| 19 |
| Pamene mumangira tsasa mudzi masiku ambiri, pouthirira nkhondo kuugwira, usamaononga mitengo yace ndi kuitema ndi nkhwangwa; pakuti ukadyeko, osailikha; pakuti mtengo wa m'munda ndiwo munthu kodi kuti uumangire tsasa? |
| 20 |
| Koma mitengo yoidziwa inu kuti si ndiyo mitengo yazipatso, imeneyi muiononge ndi kuilikha; ndipo mudzi wocita nanu nkhondo muumangire macemba, mpaka mukaugonjetsa. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/deuteronomy/020.mp3
34
20