Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Mukapenya ng'ombe kapena nkhosa ya mbale wako zilikusokera musamazilekerera, muzimbwezera mbale wanu ndithu. |
| 2 |
| Ndipo ngati mbale wanu sakhala pafupi ndi inu, kapena mukapanda kumdziwa, mubwere nayo kwanu kunyumba yanu, kuti ikhale kwanu, kufikira mbale wanu akaifuna, ndipo wambwezera iyo. |
| 3 |
| Mutero nayenso bulu wake; mutero nachonso chovala chake, mutero nachonso chotayika chilichonse cha mbale wanu, chakumtayikira mukachipeza ndi inu; musamazilekerera. |
| 4 |
| Mukapenya bulu kapena ng'ombe ya mbale wanu, zitagwa m'njira, musamazilekerera; mumthandize ndithu kuziutsanso. |
| 5 |
| Mkazi asavale chovala cha mwamuna, kapena mwamuna asavale chovala cha mkazi; pakuti aliyense wakuchita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye. |
| 6 |
| Mukachipeza chisa cha mbalame panjira, mumtengo kapena panthaka pansi, muli ana kapena mazira, ndi make alikuumatira ana kapena mazira, musamatenga make pamodzi ndi ana; |
| 7 |
| muloletu make amuke, koma mudzitengere ana; kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke. |
| 8 |
| Pamene mumanga nyumba yatsopano, muzimanga kampanda pa tsindwi lake, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu. |
| 9 |
| Musamabzala mbeu zosiyana m'munda wanu wamphesa, kuti zingaipsidwe mbeu zonse udazibzala, ndi zipatso za munda wamphesa zomwe. |
| 10 |
| Musamalima ndi bulu ndi ng'ombe zikoke pamodzi. |
| 11 |
| Musamavala nsalu yosokonezeka yaubweya pamodzi ndi thonje. |
| 12 |
| Mudzipangire mphonje pangodya zinai za chofunda chanu chimene mudzifunda nacho. |
| 13 |
| Munthu akatenga mkazi, nalowana naye, namuda, |
| 14 |
| namneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kumveketsa dzina loipa, ndi kuti, Ndinamtenga mkazi uyu, koma polowana naye sindinapeza zizindikiro zakuti ndiye namwali ndithu; |
| 15 |
| pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wake azitenga ndi kutuluka nazo zizindikiro za unamwali wake wa namwaliyo, kunka nazo kwa akulu a mudzi kuchipata; |
| 16 |
| ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akulu, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake, koma amuda; |
| 17 |
| ndipo, taonani, wamneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kuti, Sindinapeza zizindikiro za unamwali wake m'mwana wako wamkazi; koma si izi zizindikiro za unamwali wa mwana wanga wamkazi. Ndipo azifunyulula chovalacho pamaso pa akulu a mudziwo. |
| 18 |
| Pamenepo akulu a mudziwo azitenga munthuyu ndi kumkwapula; |
| 19 |
| ndi kumlipitsa masekeli makumi okhaokha khumi a siliva, ndi kuipereka kwa atate wa namwaliyo, popeza anamveketsa dzina loipa namwali wa Israele, ndipo azikhala mkazi wake, sakhoza kumchotsa masiku ake onse. |
| 20 |
| Koma chikakhala choona ichi, kuti zizindikiro zakuti ndiye namwali zidamsowa namwaliyo; |
| 21 |
| pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mudzi wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa m'Israele, kuchita chigololo m'nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu. |
| 22 |
| Akampeza munthu alikugona ndi mkazi wokwatibwa ndi mwamuna; afe onse awiri, mwamuna wakugona ndi mkazi, ndi mkazi yemwe; chotero muzichotsa choipacho mwa Israele. |
| 23 |
| Pakakhala namwali, wosadziwa mwamuna, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, ndipo anampeza m'mudzi mwamuna, nagona naye; |
| 24 |
| muziwatulutsa onse awiri kunka nao ku chipata cha mudzi uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanafuule angakhale anali m'mudzi; ndi mwamuna popeza anachepetsa mkazi wa mnansi wake; chotero muzichotsa choipacho pakati panu. |
| 25 |
| Koma mwamuna akapeza namwali wopalidwa bwenzi kuthengo, namgwira mwamunayo, nagona naye; pamenepo afe mwamuna yekha wogona naye; |
| 26 |
| koma namwaliyo musamamchitira kanthu; namwaliyo alibe tchimo loyenera imfa; pakuti mlandu uwu ukunga munthu waukira mnzake namupha; |
| 27 |
| pakuti anampeza kuthengo; namwali wopalidwa bwenziyo anafuula, koma panalibe wompulumutsa. |
| 28 |
| Munthu akapeza namwali wosadziwa mwamuna, ndiye wosapalidwa ubwenzi, nakamgwira nagona naye, napezedwa iwo, |
| 29 |
| pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wake wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wake; popeza anamchepetsa; sakhoza kumchotsa masiku ake onse. |
| 30 |
| Munthu asatenge mkazi wa atate wake, kapena kuvula atate wake. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/deuteronomy/022.mp3
34
22