Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Mose ndi akuluakulu a Israeli analamula anthu kuti, “Sungani malamulo onse amene ndikukupatsani lero lino. |
| 2 |
| Mukawoloka mtsinje wa Yorodani kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, muyimiritse miyala ingapo ikuluikulu ndi kuyikulungiza. |
| 3 |
| Mulembepo mawu onse a malamulo amenewa pamene muwoloka kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani. |
| 4 |
| Ndipo mukawoloka Yorodani muyimike miyala iyi pa Phiri la Ebala monga momwe ndikukulamulirani lero lino ndipo muyikulungize. |
| 5 |
| Pamenepo mumange guwa lansembe la miyala la Yehova Mulungu wanu. Musagwiritse ntchito chida chilichonse chachitsulo pa miyalapo. |
| 6 |
| Mumange guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu ndi miyala yakutchire ndi kuperekerapo nsembe yopsereza kwa Yehova Mulungu wanu. |
| 7 |
| Muperekerepo nsembe zopereka za chiyanjano, muzidye ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu. |
| 8 |
| Ndipo pa miyalapo mudzalembepo mawu onse a malamulo ndi malemba akuluakulu.” |
| 9 |
| Kenaka Mose ndi ansembe, amene ndi Alevi anati kwa Aisraeli onse, “Khalani chete Aisraeli inu ndipo mumvetsere! Tsopano inu ndinu anthu a Yehova Mulungu wanu. |
| 10 |
| Muzimvera Yehova Mulungu wanu ndi kutsata malamulo ake ndi malangizo ake omwe ndikukupatsani lero lino.” |
| 11 |
| Tsiku lomwelo Mose analamula anthu kuti: |
| 12 |
| Mukawoloka Yorodani, mafuko awa akayimirire pa Phiri la Gerizimu ndi kudalitsa anthu: Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini. |
| 13 |
| Ndipo mafuko awa akayimirire pa Phiri la Ebala ndi kutchula matemberero: Rubeni, Gadi, Aseri, Zebuloni, Dani ndi Nafutali. |
| 14 |
| Alevi adzayankhula mokweza kwa Aisraeli onse kuti: |
| 15 |
| “Ndi wotembereredwa munthu amene asema chifanizo kapena kupanga fano, ndi kuchiyika mobisa, pakuti chimenechi ndi chinthu chodetsedwa pamaso pa Yehova, ntchito za manja a anthu.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
| 16 |
| “Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira ulemu abambo ake kapena amayi ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
| 17 |
| “Ndi wotembereredwa munthu amene amasuntha mwala wa malire wa mnzake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
| 18 |
| “Ndi wotembereredwa munthu amene amasocheretsa munthu wosaona pa msewu.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
| 19 |
| “Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira chilungamo mlendo, ana amasiye kapena mkazi wamasiye.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
| 20 |
| “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mkazi wa abambo ake pakuti iye sachitira ulemu pogona pa abambo ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
| 21 |
| “Ndi wotembereredwa munthu amene achita chigololo ndi nyama ya mtundu uli wonse.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
| 22 |
| “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake kapena mwana wamkazi wa amayi ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
| 23 |
| “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi apongozi ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
| 24 |
| “Ndi wotembereredwa munthu amene apha mnzake mwachinsinsi.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
| 25 |
| “Ndi wotembereredwa munthu amene alandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
| 26 |
| “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita kapena sasunga mawu a malamulo awa.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/deuteronomy/027.mp3
34
27