Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Pamenepo tinatembenuka, ndi kubwera kunka njira ya ku Basani; ndipo Ogi mfumu ya Basani anatuluka kukomana nafe, kugwirana nafe nkhondo, iye ndi anthu ake onse, ku Ederei. |
| 2 |
| Ndipo Yehova anati kwa ine, Usamuopa; popeza ndampereka iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake, m'dzanja lako; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene anakhala m'Hesiboni. |
| 3 |
| Potero Yehova Mulungu wathu anaperekanso m'manja mwathu Ogi mfumu ya Basani, ndi anthu ake onse, ndipo tinamkantha kufikira sanamtsalire ndi mmodzi yense. |
| 4 |
| Ndipo muja tinalanda midzi yake yonse; kunalibe mudzi sitinaulanda m'manja mwao, midzi makumi asanu ndi limodzi, dera lonse la Arigobu, dziko la Ogi m'Basani. |
| 5 |
| Yonseyi ndiyo midzi yozinga ndi malinga atali, zitseko, ndi mipiringidzo; pamodzi ndi midzi yambirimbiri yopanda malinga. |
| 6 |
| Ndipo tinaiononga konse, monga umo tinachitira Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi kuononga konse midzi yonse, amuna, akazi ndi ana. |
| 7 |
| Koma zoweta zonse ndi zofunkha za m'midzi, tinadzifunkhira tokha. |
| 8 |
| Ndipo muja tinalanda dziko m'manja mwa mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, kuyambira mtsinje wa Arinoni kufikira phiri la Heremoni; |
| 9 |
| (Asidoni alitcha Heremoni Sirioni, koma Aamori alitcha Seniri); |
| 10 |
| midzi yonse ya kuchidikha, ndi Giliyadi lonse, ndi Basani lonse kufikira ku Saleka ndi Ederei, midzi ya dziko la Ogi m'Basani. |
| 11 |
| (Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi m'Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu). |
| 12 |
| Ndipo dziko ili tinalilanda muja; kuyambira ku Aroere, wa ku mtsinje wa Arinoni, ndi dera lina la ku mapiri a Giliyadi, ndi midzi yake, ndinapatsa Arubeni ndi Agadi. |
| 13 |
| Ndi chotsalira cha Giliyadi, ndi Basani lonse, dziko la Ogi, ndinapatsa fuko la hafu la Manase; dziko lonse la Arigobu, pamodzi ndi Basani. (Ndilo lotchedwa dziko la Arefaimu. |
| 14 |
| Yairi mwana wa Manase analanda dziko lonse la Arigobu, kufikira malire a Agesuri ndi Amaakati; nalitcha dzina lake, Basani Havoti-Yairi, kufikira lero lino). |
| 15 |
| Ndipo ndinampatsa Makiri Giliyadi. |
| 16 |
| Koma ndinapatsa Arubeni ndi Agadi kuyambira ku Giliyadi kufikira ku mtsinje wa Arinoni, pakati pa chigwa ndi malire ake, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni; |
| 17 |
| ndi chidikha, ndi Yordani ndi malire ake, kuyambira ku Kinereti kufikira ku Nyanja ya Araba, ndiyo Nyanja ya Mchere, patsinde pa Pisiga, kum'mawa. |
| 18 |
| Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanulanu, muoloke, amuna onse amphamvu ovala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israele. |
| 19 |
| Koma akazi anu, ndi ana anu, ndi zoweta zanu, (ndidziwa muli nazo zoweta zambiri), zikhale m'midzi yanu imene ndinakupatsani; |
| 20 |
| kufikira Yehova atapumulitsa abale anu, monga anapumulitsa inu, nalandira iwonso dziko limene Yehova Mulungu wanu awapatsa tsidya lija la Yordani; pamenepo mudzabwerera munthu yense ku cholowa chake, chimene ndinakupatsani. |
| 21 |
| Ndipo ndinauza Yoswa muja, ndi kuti, Maso ako anapenya zonse Yehova Mulungu wanu anawachitira mafumu awa awiri; momwemo Yehova adzachitira maufumu onse kumene muolokerako. |
| 22 |
| Musawaopa popeza Yehova Mulungu wanu, ndiye agwirira inu nkhondo. |
| 23 |
| Ndipo ndinapempha chifundo kwa Yehova nthawi yomwe ija, ndi kuti, |
| 24 |
| Ambuye Yehova, mwayamba Inu kuonetsera mtumiki wanu ukulu wanu, ndi dzanja lanu lamphamvu; pakuti Mulungu ndani m'mwamba kapena pa dziko lapansi wakuchita monga mwa ntchito zanu, ndi monga mwa mphamvu zanu? |
| 25 |
| Ndioloketu, ndilione dziko lokomali lili tsidya la Yordani, mapiri okoma aja, ndi Lebanoni. |
| 26 |
| Koma Yehova anakwiya ndi ine, chifukwa cha inu, sanandimvere ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Chikukwanire, usaonjezenso kunena ndi Ine za chinthuchi. |
| 27 |
| Kwera kumwamba ku Pisiga, nukweze maso ako kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, ndi kum'mawa, nuyang'ane ndi maso ako; popeza sudzaoloka Yordani uyo. |
| 28 |
| Koma langiza Yoswa, numlimbitse mtima, ndi kumkhwimitsa, pakuti adzaoloka pamaso pa anthu awa, nadzawalandiritsa dziko ulionali likhale laolao. |
| 29 |
| Potero tinakhala m'chigwamo pandunji pa Betepeori. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/deuteronomy/003.mp3
34
3