Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Kumwamba kutchere khutu, ndipo ndidzanena; ndi dziko lapansi limve mau a m'kamwa mwanga. |
| 2 |
| Chiphunzitso changa chikhale ngati mvula; maneno anga agwe ngati mame; ngati mvula yowaza pamsipu, ndi monga madontho a mvula pazitsamba. |
| 3 |
| Pakuti ndidzalalika dzina la Yehova. Nenani kuti Mulungu wathu ndi wamkulu. |
| 4 |
| Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika. |
| 5 |
| Anamchitira zovunda si ndiwo ana ake, chilema nchao; iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota. |
| 6 |
| Kodi mubwezera Yehova chotero, anthu inu opusa ndi opanda nzeru? Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuye wanu; anakulengani, nakukhazikitsani? |
| 7 |
| Kumbukirani masiku akale, zindikirani zaka za mibadwo yambiri; funsani atate wanu, adzakufotokozerani; akulu anu, adzakuuzani. |
| 8 |
| Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu cholowa chao, pamene anagawa ana a anthu, anaika malire a mitundu ya anthu, monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israele. |
| 9 |
| Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake; Yakobo ndiye muyeso wa cholowa chake. |
| 10 |
| Anampeza m'dziko la mabwinja, m'chipululu cholira chopanda kanthu; anamzinga, anamlangiza, anamsunga ngati kamwana ka m'diso. |
| 11 |
| Monga mphungu ikasula chisa chake, nikapakapa pa ana ake, Iye anayala mapiko ake, nawalandira, nawanyamula pa mapiko ake. |
| 12 |
| Yehova yekha anamtsogolera, ndipo palibe mulungu wachilendo naye. |
| 13 |
| Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi, ndipo anadya zipatso za m'minda; namyamwitsa uchi wa m'thanthwe, ndi mafuta m'mwala wansangalabwe; |
| 14 |
| mafuta a mkaka wang'ombe, ndi mkaka wankhosa, ndi mafuta a anaankhosa, ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basani, ndi atonde, ndi impso zonenepa zatirigu; ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa. |
| 15 |
| Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, napeputsa thanthwe la chipulumutso chake. |
| 16 |
| Anamchititsa nsanje ndi milungu yachilendo, anautsa mkwiyo wake ndi zonyansa. |
| 17 |
| Anaziphera nsembe ziwanda, si ndizo Mulungu ai; milungu yosadziwa iwo, yatsopano yofuma pafupi, imene makolo anu sanaiope. |
| 18 |
| Mwaleka Thanthwe limene linakubalani, mwaiwala Mulungu amene anakulengani. |
| 19 |
| Ndipo Yehova anachiona, nawanyoza, pakuipidwa nao ana ake amuna, ndi akazi. |
| 20 |
| Ndipo Iye anati, Ndidzawabisira nkhope yanga, ndidzaona kutsiriza kwao; popeza iwo ndiwo mbadwo wopulukira, ana osakhulupirika iwo. |
| 21 |
| Anautsa nsanje yanga ndi chinthu chosati Mulungu; anautsa mkwiyo wanga ndi zopanda pake zao. Ndidzautsa nsanje yao ndi iwo osakhala mtundu wa anthu; ndidzautsa mkwiyo wao ndi mtundu wa anthu opusa. |
| 22 |
| Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga, utentha kumanda kunsi ukutha dziko lapansi ndi zipatso zake, nuyatsa maziko a mapiri. |
| 23 |
| Ndidzawaunjikira zoipa; ndidzawathera mivi yanga. |
| 24 |
| Adzaonda nayo njala adzanyekeka ndi makala a moto, chionongeko chowawa; ndipo ndidzawatumizira mano a zilombo, ndi ululu wa zokwawa m'fumbi. |
| 25 |
| Pabwalo lupanga lidzalanda, ndi m'zipinda mantha; lidzaononga mnyamata ndi namwali, woyamwa pamodzi ndi munthu waimvi. |
| 26 |
| Ndinati, Ndikadawauzira ndithu, ndikadafafaniza chikumbukiro chao mwa anthu. |
| 27 |
| Ndikadapanda kuopa mkwiyo wa pa mdani, angayese molakwa outsana nao, anganene, Lakwezeka dzanja lathu, ndipo Yehova sanachite ichi chonse. |
| 28 |
| Popeza iwo ndiwo mtundu wa anthu wosowa uphungu konse, ndipo alibe chidziwitso. |
| 29 |
| Akadakhala nazo nzeru, akadazindikira ichi, akadasamalira chitsirizo chao! |
| 30 |
| Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova. |
| 31 |
| Popeza thanthwe lao nlosanga Thanthwe lathu, oweruza a pamenepo ndiwo adani athu. |
| 32 |
| Pakuti mpesa wao ndiwo wa ku Sodomu, ndi wa m'minda ya ku Gomora; mphesa zao ndizo mphesa zandulu, matsangwi ao ngowawa. |
| 33 |
| Vinyo wao ndiwo ululu wa zinjoka, ndi ululu waukali wa mphiri. |
| 34 |
| Kodi sichisungika ndi Ine, cholembedwa chizindikiro mwa chuma changa chenicheni? |
| 35 |
| Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe, pa nyengo ya kuterereka phazi lao; pakuti tsiku la tsoka lao layandika, ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza. |
| 36 |
| Popeza Yehova adzaweruza anthu ake, nadzachitira nsoni anthu ake; pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha, wosatsala womangika kapena waufulu. |
| 37 |
| Pamenepo adzati, Ili kuti milungu yao, thanthwe limene anathawirako? |
| 38 |
| Imene inadya mafuta a nsembe zao zophera, nimwa vinyo wa nsembe yao yothira? Iuke nikuthandizeni, Ikhale pobisalapo panu. |
| 39 |
| Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa. |
| 40 |
| Pakuti ndikweza dzanja langa kuloza kumwamba, ndipo nditi, Pali moyo wanga kosatha, |
| 41 |
| ndikanola lupanga langa lonyezimira, ndi dzanja langa likagwira chiweruzo; ndidzabwezera chilango ondiukira, ndi kulanga ondida. |
| 42 |
| Mivi yanga ndiiledzeretsa nao mwazi, ndi lupanga langa lidzalusira nyama; ndi mwazi wa ophedwa ndi ogwidwa, ndi mutu wachitsitsi wa mdani. |
| 43 |
| Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake; adzalipsira mwazi wa atumiki ake, adzabwezera chilango akumuukira, nadzafafanizira zoipa dziko lake, ndi anthu ake. |
| 44 |
| Ndipo anadza Mose nanena mau onse a nyimbo iyi m'makutu mwa anthu, iye, ndi Yoswa mwana wa Nuni. |
| 45 |
| Ndipo Mose anatha kunena mau awa onse kwa Israele wonse; |
| 46 |
| nati nao, Ikani mitima yanu pa mau onse ndikuchitirani nao mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mau onse a chilamulo ichi. |
| 47 |
| Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu, ndipo mwa chinthu ichi mudzachulukitsa masiku anu m'dziko limene muolokera Yordani, kulilandira. |
| 48 |
| Ndipo Yehova ananena ndi Mose tsiku lomweli, ndi kuti, |
| 49 |
| Kwera m'phiri muno mwa Abarimu, phiri la Nebo, lokhala m'dziko la Mowabu, popenyana ndi Yeriko; nupenye dziko la Kanani, limene ndipereka kwa ana a Israele likhale laolao; |
| 50 |
| nufe m'phiri m'mene ukweramo, nuitanidwe kunka kwa anthu a mtundu wako; monga Aroni mbale wako anafa m'phiri la Hori, naitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; |
| 51 |
| popeza munandilakwira pakati pa ana a Israele ku madzi a Meriba wa Kadesi m'chipululu cha Zini, popeza simunandipatula Ine pakati pa ana a Israele. |
| 52 |
| Pakuti udzapenya dzikoli pandunji pako; koma osalowako ku dziko limene ndipatsa ana a Israele. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/deuteronomy/032.mp3
34
32