Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo Mose anakwera kuchokera ku zidikha za Mowabu, kunka kuphiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Giliyadi, kufikira ku Dani; |
| 2 |
| ndi Nafutali lonse, ndi dziko la Efuremu, ndi Manase, ndi dziko lonse la Yuda, kufikira nyanja ya m'tsogolo; |
| 3 |
| ndi kumwera, ndi chidikha cha chigwa cha Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kufikira ku Zowari. |
| 4 |
| Ndipo Yehova anati kwa iye, Si ili dziko ndinalumbirira Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzalipereka kwa mbeu zako. Ndinakuonetsa ili m'maso, koma sudzaolokako. |
| 5 |
| Ndipo Mose mtumiki wa Yehova anamwalirako m'dziko la Mowabu, monga mwa mau a Yehova. |
| 6 |
| Ndipo Iye anamuika m'chigwa m'dziko la Mowabu popenyana ndi Betepeori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwake kufikira lero lino. |
| 7 |
| Ndipo zaka zake za Mose ndizo zana limodzi ndi makumi awiri, pakumwalira iye; diso lake silinachita mdima, ndi mphamvu yake siidaleka. |
| 8 |
| Ndipo ana a Israele analira Mose m'zidikha za Mowabu masiku makumi atatu; potero anatha masiku akulira maliro a Mose. |
| 9 |
| Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anadzala ndi mzimu wanzeru; popeza Mose adamuikira manja ake; ndi ana a Israele anamvera iye, nachita monga Yehova adauza Mose. |
| 10 |
| Ndipo sanaukenso mneneri m'Israele ngati Mose, amene Yehova anadziwana naye popenyana maso; |
| 11 |
| kunena za zizindikiro ndi zozizwa zonse zimene Yehova anamtumiza kuzichita m'dziko la Ejipito kwa Farao, ndi anyamata ake onse, ndi dziko lake lonse; |
| 12 |
| ndi kunena za dzanja la mphamvu lonse, ndi choopsa chachikulu chonse, chimene Mose anachita pamaso pa Israele wonse. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/deuteronomy/034.mp3
34
34