Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo awa ndi malamulo, malemba, ndi maweruzo, amene Yehova Mulungu wanu analamulira kukuphunzitsani, kuti muziwachita m'dziko limene muolokerako kulilandira; |
| 2 |
| kuti muope Yehova Mulungu wanu, kusunga malemba ake onse ndi malamulo ake, amene ndikuuzani inu ndi ana anu, ndi zidzukulu zanu, masiku onse a moyo wanu, ndi kuti masiku anu achuluke. |
| 3 |
| Potero imvani, Israele, musamalire kuwachita, kuti chikukomereni ndi kuti muchuluke chichulukire, monga Yehova Mulungu wa makolo anu anena ndi inu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. |
| 4 |
| Imvani, Israele; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi; |
| 5 |
| ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse. |
| 6 |
| Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; |
| 7 |
| ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu. |
| 8 |
| Ndipo muziwamanga padzanja panu ngati chizindikiro, ndipo akhale ngati chapamphumi pakati pa maso anu. |
| 9 |
| Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu. |
| 10 |
| Ndipo kudzakhala, Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuti adzakupatsani ili; midzi yaikulu ndi yokoma, imene simunaimanga; |
| 11 |
| ndi nyumba zodzala nazo zokoma zilizonse, zimene simunazidzaza, ndi zitsime zosema, zimene simunazisema, minda yampesa, ndi minda ya azitona, zimene simunazioka, ndipo mutakadya ndi kukhuta; |
| 12 |
| pamenepo mudzichenjere mungaiwale Yehova, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya akapolo. |
| 13 |
| Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzitchula dzina lake. |
| 14 |
| Musamatsata milungu ina, milungu ina ya mitundu ya anthu akuzinga inu; |
| 15 |
| pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukuchotsani pankhope pa dziko lapansi. |
| 16 |
| Musamayesa Yehova Mulungu wanu, monga munamyesa m'Masa. |
| 17 |
| Muzisunga mwachangu malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi mboni zake, ndi malemba ake, amene anakulamulirani. |
| 18 |
| Ndipo muzichita zolunjika ndi zokoma pamaso pa Yehova; kuti chikukomereni, ndi kuti mulowe kukalandira dziko lokomali Yehova analumbirira makolo anu, |
| 19 |
| kuingitsa adani anu onse pamaso panu, monga Yehova adanena. |
| 20 |
| Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Mbonizo, ndi malemba, ndi maweruzo, zimene Yehova Mulungu wathu anakulamulirani, zitani? |
| 21 |
| Pamenepo muzinena kwa ana anu, Tinali akapolo a Farao m'Ejipito; ndipo Yehova anatitulutsa m'Ejipito ndi dzanja lamphamvu. |
| 22 |
| Ndipo Yehova anapatsa zizindikiro ndi zozizwa zazikulu ndi zowawa m'Ejipito, pa Farao, ndi pa nyumba yake yonse, pamaso pathu; |
| 23 |
| ndipo anatitulutsa komweko, kuti atilowetse, kutipatsa dzikoli analumbirira makolo athu. |
| 24 |
| Ndipo Yehova anatilamulira tizichita malemba awa onse, kuopa Yehova Mulungu wathu, kuti tipindule nako masiku onse, kuti atisunge amoyo, monga lero lino. |
| 25 |
| Ndipo kudzakhala kwa ife chilungamo, ngati tisamalira kuchita malamulo awa onse pamaso pa Yehova Mulungu wathu, monga anatilamulira ife. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/deuteronomy/006.mp3
34
6