Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Pakuti, abale, mudziwa nokha malowedwe athu a kwa inu, kuti sanakhala opanda pace; |
| 2 |
| koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anaticitira cipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri. |
| 3 |
| Pakuti kudandaulira kwathu sikucokera kukusocera, kapena kucidetso, kapena m'dnyengo; |
| 4 |
| komatu monga Mulungu anatibvomereza kutiikiza Uthenga Wabwino, kotero tilankhula; osati monga okondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu. |
| 5 |
| Pakuti sitinayenda nao mau osyasyalika nthawi iri yonse, monga mudziwa, kapena kupsiniira msiriro, mboni ndi Mulungu; |
| 6 |
| kapena sitinakhala ofuna ulemerero wa kwa anthu, kapena kwa inu, kapena kwa ena, tingakhale tinali nayo mphamvu yakukulemetsanl monga atumwi a Kristu. |
| 7 |
| Komatu tinakhala ofat sa pakati pa inu, monga m'mene mlezi afukata ana ace a iye yekha; |
| 8 |
| kotero ife poliralira inu, tinabvomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife. |
| 9 |
| Pakuti mukumbukila, abale, cigwiritso cathu ndi cibvuto cathu; pocita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu. |
| 10 |
| Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira; |
| 11 |
| monga mudziwa kuti tinacitira yense wa inu pa yekha, monga atate acitira ana ace a iye yekha, ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kucita umboni, |
| 12 |
| kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wace wa iye yekha, ndi ulemerero. |
| 13 |
| Ndipo mwa icinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso acita mwa inuokhulupirira. |
| 14 |
| Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m'Yudeya mwa Kristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa nelinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowapa manja a Ayuda; |
| 15 |
| amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri, natilondalonda ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nao anthu onse; |
| 16 |
| natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza macimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira cimariziro. |
| 17 |
| Koma ife, abale, angakhale adaticotsa kusiyana nanu kanthawi, osapenyana maso, koma kusiyana mtima ai, tinayesetsa koposa kuona nkhope yanu ndi cilakolako cacikuru; |
| 18 |
| cifukwa tinafuna kudza kwa inu, inedi Paulo ndatero kamodzi kapena kawiri; koma Satana anatiletsa. |
| 19 |
| Pakuti ciyembekezo cathu, kapena cimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nciani? si ndinu nanga pamaso pa Ambuye wathu Yesu m'kufika kwace? |
| 20 |
| Pakuti inu ndinu ulemerero wathu ndi cimwemwe cathu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/1thessalonians/002.mp3
5
2