Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Chifukwa chake, posakhoza kulekereranso, tidavomereza mtima atisiye tokha ku Atene; |
| 2 |
| ndipo tinatuma Timoteo, mbale wathuyo ndi mtumiki wa Mulungu m'Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti akhazikitse inu, ndi kutonthoza inu za chikhulupiriro chanu; |
| 3 |
| kuti asasunthike wina ndi zisautso izi, pakuti mudziwa nokha kuti adatiika ife tichite izi. |
| 4 |
| Pakutinso, pamene tinali ndi inu tinakuuziranitu kuti tidzamva zisautso; monga kudachitika, monganso mudziwa. |
| 5 |
| Mwa ichi inenso, posalekereranso, ndinatuma kukazindikira chikhulupiriro chanu, kuti kapena woyesa akadakuyesani, ndipo chivuto chathu chikadakhala chopanda pake. |
| 6 |
| Koma tsopano pofika Timoteo kwathu kuchokera kwa inu, ndi kutifotokozera mbiri yokoma ya chikhulupiriro ndi chikondano chanu, ndi kuti mutikumbukira bwino masiku onse, pokhumba kutiona ife, monganso ife kukuonani inu; |
| 7 |
| chifukwa cha ichi tasangalala pa inu, abale, m'kupsinjika kwathu konse ndi chisautso chathu chonse, mwa chikhulupiriro chanu; |
| 8 |
| pakuti tsopano tili ndi moyo, ngati inu muchilimika mwa Ambuye. |
| 9 |
| Pakuti tikhoza kubwezera kwa Mulungu chiyamiko chanji chifukwa cha inu, pa chimwemwe chonse tikondwera nacho mwa inu pamaso pa Mulungu wathu; |
| 10 |
| ndi kuchulukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikaone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewera pa chikhulupiriro chanu? |
| 11 |
| Koma Mulungu Atate wathu mwini yekha, ndi Ambuye wathu Yesu atitsogolere m'njira yakufika kwa inu; |
| 12 |
| koma Ambuye akukulitseni inu, nakuchulukitseni m'chikondano wina kwa mnzake ndi kwa anthu onse, monganso ife titero kwa inu; |
| 13 |
| kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda chifukwa m'chiyero pamaso pa Mulungu Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu pamodzi ndi oyera mtima ake onse. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/1thessalonians/003.mp3
5
3