Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo. |
| 2 |
| Pakuti mudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa Ambuye Yesu. |
| 3 |
| Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama; |
| 4 |
| yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m'chiyeretso ndi ulemu, |
| 5 |
| kosati m'chiliro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu; |
| 6 |
| asapitirireko munthu, nanyenge mbale wake m'menemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinachitapo umboni. |
| 7 |
| Pakuti Mulungu sanaitana ife titsate chidetso, koma chiyeretso. |
| 8 |
| Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu. |
| 9 |
| Koma kunena za chikondano cha pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake; |
| 10 |
| pakutinso munawachitira ichi abale onse a m'Masedoniya lonse. Koma tikudandaulirani, abale, muchulukireko koposa, |
| 11 |
| ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani; |
| 12 |
| kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu. |
| 13 |
| Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo. |
| 14 |
| Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu. |
| 15 |
| Pakuti ichi tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo. |
| 16 |
| Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mau a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Khristu adzayamba kuuka; |
| 17 |
| pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse. |
| 18 |
| Chomwecho, tonthozanani ndi mau awa. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/1thessalonians/004.mp3
5
4