Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulemberani. |
| 2 |
| Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku. |
| 3 |
| Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse. |
| 4 |
| Koma inu, abale, simuli mumdima, kuti tsikulo likakugwereni monga mbala; |
| 5 |
| pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; sitili a usiku, kapena a mdima; |
| 6 |
| chifukwa chake tsono tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere. |
| 7 |
| Pakuti iwo akugona agona usiku; ndi iwo akuledzera aledzera usiku. |
| 8 |
| Koma ife popeza tili a usana tisaledzere, titavala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso. |
| 9 |
| Pakuti Mulungu sanatiika ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire chipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, |
| 10 |
| amene anafa m'malo mwathu, kuti, tingakhale tidikira, tingakhale tigona, tikakhale ndi moyo pamodzi ndi Iye. |
| 11 |
| Mwa ichi chenjezanani, ndipo mangiriranani wina ndi mnzake, monganso mumachita. |
| 12 |
| Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu; |
| 13 |
| ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha. |
| 14 |
| Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima? Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse. |
| 15 |
| Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse. |
| 16 |
| Kondwerani nthawi zonse; |
| 17 |
| Pempherani kosaleka; |
| 18 |
| M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu. |
| 19 |
| Musazime Mzimuyo; |
| 20 |
| Musanyoze manenero; |
| 21 |
| Yesani zonse; sungani chokomacho, |
| 22 |
| Mupewe maonekedwe onse a choipa. |
| 23 |
| Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. |
| 24 |
| Wakuitana inu ali wokhulupirika, amenenso adzachichita. |
| 25 |
| Abale, tipempherereni ife. |
| 26 |
| Perekani moni kwa abale onse ndi chipsompsono chopatulika. |
| 27 |
| Ndikulumbirirani pa Ambuye kuti kalatayu awerengedwe kwa abale onse. |
| 28 |
| Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale nanu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/1thessalonians/005.mp3
5
5