Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Tsono abale, za nthawi ndi nyengo yake nʼkosafunikira kuti tikulembereni, |
| 2 |
| chifukwa mukudziwa bwino lomwe kuti tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala usiku. |
| 3 |
| Pamene anthu akunena kuti, “Mtendere ndi chitetezo,” chiwonongeko chidzafika pa iwo mwadzidzidzi, monga zowawa za amayi pobereka, ndipo sadzathawa. |
| 4 |
| Koma inu abale, simuli mu mdima kuti tsiku limeneli lidzakudzidzimutseni ngati mbala. |
| 5 |
| Nonse ndinu ana a kuwunika ndi ana a usana. Sindife anthu a usiku kapena mdima. |
| 6 |
| Chomwecho tsono, tisafanane ndi ena amene akugona koma tikhale maso ndi odzisunga. |
| 7 |
| Pakuti amene akugona, amagona usiku, ndi amene amaledzera, amaledzera usiku. |
| 8 |
| Koma popeza ndife a usana, tikhale odzisunga, titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala pachifuwa, ndi chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa. |
| 9 |
| Pakuti Mulungu sanatisankhe kuti tikavutike ndi mkwiyo koma kuti tilandire chipulumutso kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. |
| 10 |
| Iye anatifera ndi cholinga chakuti, kaya tili ndi moyo kapena tagona, tikhale naye pamodzi. |
| 11 |
| Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira. |
| 12 |
| Tsopano tikukupemphani abale kuti muziwalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene amakuyangʼanirani mwa Ambuye ndi amene amakulimbikitsani. |
| 13 |
| Muziwachitira ulemu kwambiri mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo. Mukhale pa mtendere wina ndi mnzake. |
| 14 |
| Ndipo tikukupemphani abale, muwachenjeze amene akungokhala osagwira ntchito, alimbikitseni amanyazi, thandizani ofowoka ndipo muzilezera mtima aliyense. |
| 15 |
| Onetsetsani kuti wina asabwezere choyipa kwa omuchitira choyipa koma nthawi zonse yesetsani kukhala okoma mtima kwa wina ndi mnzake; ndiponso ndi kwa anthu ena onse. |
| 16 |
| Kondwerani nthawi zonse. |
| 17 |
| Pempherani kosalekeza. |
| 18 |
| Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu. |
| 19 |
| Musazimitse moto wa Mzimu Woyera. |
| 20 |
| Musanyoze mawu a uneneri. |
| 21 |
| Yesani zinthu zonse. Gwiritsitsani chimene ndi chabwino. |
| 22 |
| Mupewe choyipa cha mtundu wina uliwonse. |
| 23 |
| Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu. |
| 24 |
| Amene anakuyitanani ndi wokhulupirika ndipo Iye adzachita zimenezi. |
| 25 |
| Abale, mutipempherere. |
| 26 |
| Perekani moni wachikondi kwa onse. |
| 27 |
| Pamaso pa Ambuye ndikulamula kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse. |
| 28 |
| Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale nanu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/1thessalonians/005.mp3
5
5