Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo tikupemphani, abale, cifukwa ca kudza kwace kwa Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa iye; |
| 2 |
| kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika; |
| 3 |
| munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma ciyambe cifike cipatukoco, nabvumbulutsike munthu wosayeruzika, mwana wa cionongeko, |
| 4 |
| amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zochedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhalapansi ku Kacisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu. |
| 5 |
| Simukumbukila kodi, kuti pokhala nanu, ndisanacoke ine, ndinakuuzani izi? |
| 6 |
| Ndipo tsopano comletsa mucidziwa, kuti akabvumbulutsidwe iye m'nyengo yace ya iye yekha. |
| 7 |
| Pakuti cinsinsi ca kusayeruzika cayambadi kucita; cokhaci pali womletsa tsopano, kufikira akamcotsa pakati. |
| 8 |
| Ndipo pamenepo adzabvumbulutsidwa wosayeruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pace, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwace; |
| 9 |
| ndiye amene kudza kwace kuli monga mwa macitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikilo ndi zozizwa zonama; |
| 10 |
| ndi m'cinyengo conse ca cosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza cikondi ca coonadi sanacisandira, kuti akapulumutsidwe iwo. |
| 11 |
| Ndipo cifukwa cace Mulungu atumiza kwa iwo macitidwe a kusoceretsa, kuti akhulupirire bodza; |
| 12 |
| kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirira coonadi, komatu anakondwera ndi cosalungama. |
| 13 |
| Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa: ca inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira paciyambi, mulandire cipulumutso mwa ciyeretso ca Mzimu ndi cikhulupiriro ca coonadi; |
| 14 |
| kumene aoaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Kristu. |
| 15 |
| Cifukwa cace tsono, abale, cirimikani, gwiritsani miyambo imene tinakuphunzitsani, kapena mwa mau, kapena mwa kalata wathu. |
| 16 |
| Ndipo Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa elsangalatso cosatha ndi ciyembekezo cokoma mwa cisomo, |
| 17 |
| asangalatse mitima yanu, nakhazikitse inu mu nchito yonse ndi mau onse abwino. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/2thessalonians/002.mp3
3
2