Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo tikupemphani, abale, chifukwa cha kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa Iye; |
| 2 |
| kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika; |
| 3 |
| munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chifike chipatukocho, navumbulutsike munthu wosaweruzika, mwana wa chionongeko, |
| 4 |
| amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu. |
| 5 |
| Simukumbukira kodi, kuti pokhala nanu, ndisanachoke ine, ndinakuuzani izi? |
| 6 |
| Ndipo tsopano chomletsa muchidziwa, kuti akavumbulitsidwe iye m'nyengo yake ya iye yekha. |
| 7 |
| Pakuti chinsinsi cha kusaweruzika chayambadi kuchita; chokhachi pali womletsa tsopano, kufikira akamchotsa pakati. |
| 8 |
| Ndipo pamenepo adzavumbulutsidwa wosaweruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pake, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwake; |
| 9 |
| ndiye amene kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama; |
| 10 |
| ndi m'chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza chikondi cha choonadi sanachilandira, kuti akapulumutsidwe iwo. |
| 11 |
| Ndipo chifukwa chake Mulungu atumiza kwa iwo machitidwe a kusocheretsa, kuti akhulupirire bodza; |
| 12 |
| kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirira choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama. |
| 13 |
| Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira pachiyambi, mulandire chipulumutso mwa chiyeretso cha Mzimu ndi chikhulupiriro cha choonadi; |
| 14 |
| kumene anaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu. |
| 15 |
| Chifukwa chake tsono, abale, chilimikani, gwiritsani miyambo imene tinakuphunzitsani, kapena mwa mau, kapena mwa kalata wathu. |
| 16 |
| Ndipo Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo, |
| 17 |
| asangalatse mitima yanu, nakhazikitse inu mu ntchito yonse ndi mau onse abwino. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/2thessalonians/002.mp3
3
2