Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Chotsalira, abale, mutipempherere, kuti mau a Ambuye athamange, nalemekezedwe, monganso kwanu; |
| 2 |
| ndi kuti tilanditsidwe m'manja a anthu osayenera ndi oipa; pakuti si onse ali nacho chikhulupiriro. |
| 3 |
| Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo; |
| 4 |
| koma tikhulupirira mwa Ambuye za inu, kuti mumachita, ndiponso mudzachita zimene tikulamulirani. |
| 5 |
| Ndipo Ambuye atsogolere bwino mitima yanu ilowe m'chikondi cha mulungu ndi m'chipiriro cha Khristu. |
| 6 |
| Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife. |
| 7 |
| Pakuti mudziwa nokha m'mene muyenera kutitsanza ifemo; pakuti sitinakhala dwakedwake mwa inu; |
| 8 |
| kapena sitinadya mkate chabe pa dzanja la munthu aliyense, komatu m'chivuto ndi chipsinjo, tinagwira ntchito usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu; |
| 9 |
| si chifukwa tilibe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu chitsanzo chanu, kuti mukatitsanze ife. |
| 10 |
| Pakutinso pamene tinali nanu tidakulamulirani ichi, Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso. |
| 11 |
| Pakuti tikumva za ena mwa inu kuti ayenda dwakedwake, osagwira ntchito konse, koma ali ochita mwina ndi mwina. |
| 12 |
| Koma oterewa tiwalamulira ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Khristu, kuti agwire ntchito pokhala chete, nadye chakudya cha iwo okha. |
| 13 |
| Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino. |
| 14 |
| Koma ngati wina samvera mau athu m'kalata uyu, yang'anirani ameneyo, kuti musayanjane naye, kuti achite manyazi. |
| 15 |
| Koma musamuyese mdani, koma mumuyambirire ngati mbale. |
| 16 |
| Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse, monsemo. Ambuye akhale ndi inu nonse. |
| 17 |
| Ndipereka moni ndi dzanja langa Paulo; ndicho chizindikiro m'kalata aliyense; ndiko kulemba kwanga. |
| 18 |
| Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/2thessalonians/003.mp3
3
3