|
| 1 |
|
| Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika. |
|
| 2 |
|
| Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima. |
|
| 3 |
|
| Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu, |
|
| 4 |
|
| amene amafuna kuti anthu onse apulumutsidwe ndipo kuti adziwe choonadi. |
|
| 5 |
|
| Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu. |
|
| 6 |
|
| Iyeyu anadzipereka kukhala dipo lowombolera anthu onse. Umenewu ndi umboni umene waperekedwa mu nthawi yake yoyenera. |
|
| 7 |
|
| Nʼchifukwa chake anandisankha kukhala mlaliki ndiponso mtumwi wophunzitsa anthu a mitundu ina mawu achikhulupiriro choona. Sindikunama ayi, ndikunena zoona. |
|
| 8 |
|
| Choncho ndikufuna kuti paliponse popemphera, amuna azikweza manja awo kwa Mulungu mopanda mkwiyo kapena kukangana. |
|
| 9 |
|
| Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali. |
|
| 10 |
|
| Koma adzikongoletse ndi ntchito zabwino zoyenera mayi wopembedza Mulungu. |
|
| 11 |
|
| Amayi azikhala chete pophunzitsidwa ndi mtima ogonjera kwathunthu. |
|
| 12 |
|
| Ine sindikulola kuti amayi aziphunzitsa kapena kulamulira amuna; koma akhale chete. |
|
| 13 |
|
| Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa kenaka Hava. |
|
| 14 |
|
| Ndipo Adamu si amene ananyengedwa koma mkazi ndiye amene ananyengedwa nachimwa. |
|
| 15 |
|
| Ndipo mkazi adzapulumutsidwa pobereka mwana ngati apitiriza kukhala mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkuyera mtima pamodzi ndi kudzichepetsa konse. |
|
|
|
|