Ndine, Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Adandituma kuti amene Mulungu adaŵasankha, ndiŵatsogolere ku chikhulupiriro, azizindikira choona chimene chimaŵafikitsa ku moyo wolemekeza Mulungu,
Ndikulembera iwe Tito, mwana wanga weniweni chifukwa choti ineyo ndi iwe tili m'chikhulupiriro chimodzimodzi. Mulungu Atate ndi Khristu Yesu, Mpulumutsi wathu, akukomere mtima ndi kukupatsa mtendere.
Asunge mogwiritsa mau okhulupirika, amene ali ogwirizana ndi zimene tidaphunzitsidwa. Pakutero adzatha kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona, ndiponso kugonjetsa otsutsana nacho.
Kwa anthu oyera mtima, zinthu zonse nzoyera. Koma kwa amene ali odetsedwa ndi osakhulupirira, palibe kanthu koyera; mitima yao ndi nzeru zao zomwe, zonse nzodetsedwa.
Amatsimikiza kuti amadziŵa Mulungu, pamene ndi zochita zao amamkana, pakuti ndi anthu onyansa osamvera, ndi osayenera kuchita kanthu kalikonse kabwino.