Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Koma iwe, lankhula zimene ziyenera ciphunzitso colamitsa: |
| 2 |
| okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m'cikhulupiriro, m'cikondi, m'cipiriro. |
| 3 |
| Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa naco cikondi ca pavinyo, akuphunzitsa zokoma; |
| 4 |
| kuti akalangize akazi ang one akonde amuna ao, akonde ana ao, |
| 5 |
| akhale odziletsa, odekha, ocita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angacitidwe mwano. |
| 6 |
| Momwemonso anyamata uwadandaulire akhale odziletsa; |
| 7 |
| m'zonse udzionetsere wekha citsanzo ca nchito zabwino; m'ciphunzitse cako uonetsere cosabvunda, ulemekezeko, |
| 8 |
| mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana acite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife. |
| 9 |
| Akapolo amvere ambuye ao a iwo okha, nawakondweretse m'zonse; osakana mau ao; |
| 10 |
| osatapa pa zao, komatu aonetsere cikhulupiriko conse cabwino; kuti akakometsere ciphunzitso ca Mpulumutsi wathu Mulungu m'zinthu zonse. |
| 11 |
| Pakuti caonekera cisomo ca Mulungu cakupulumutsa anthu onse, |
| 12 |
| ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana cisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza; |
| 13 |
| akulindira ciyembekezo eodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkuru ndi Mpulumutsi wathu Yesu Kristu; |
| 14 |
| amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole Ife ku zoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ace eni eni, acangu pa nchito zokoma. |
| 15 |
| Izi lankhula, ndipo ucenjeze, nudzudzule ndi ulamuliro wonse. Munthu asakupeputse. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/titus/002.mp3
3
2