Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Koma iwe, lankhula zimene ziyenera chiphunzitso cholamitsa: |
| 2 |
| okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m'chikhulupiriro, m'chikondi, m'chipiriro. |
| 3 |
| Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma; |
| 4 |
| kuti akalangize akazi aang'ono akonde amuna ao, akonde ana ao, |
| 5 |
| akhale odziletsa, odekha, ochita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angachitidwe mwano. |
| 6 |
| Momwemonso anyamata uwadandaulire akhale odziletsa; |
| 7 |
| m'zonse udzionetsere wekha chitsanzo cha ntchito zabwino; m'chiphunzitso chako uonetsere chosavunda, ulemekezeko, |
| 8 |
| mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana achite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife. |
| 9 |
| Akapolo amvere ambuye ao a iwo okha, nawakondweretse m'zonse; osakana mau ao; |
| 10 |
| osatapa pa zao, komatu aonetsere chikhulupiriko chonse chabwino; kuti akakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m'zinthu zonse. |
| 11 |
| Pakuti chaonekera chisomo cha Mulungu chakupulumutsa anthu onse, |
| 12 |
| ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza; |
| 13 |
| akulindira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu; |
| 14 |
| amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma. |
| 15 |
| Izi lankhula, ndipo uchenjeze, nudzudzule ndi ulamuliro wonse. Munthu asakupeputse. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/titus/002.mp3
3
2