Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| KALE Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyana-siyana, |
| 2 |
| koma pakutha pace pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am'mwamba omwe; |
| 3 |
| ameneyo, pokhala ali cinyezimiro ca ulemerero wace, ndi cizindikilo ceni ceni ca cikhalidwe cace, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yace, m'mene adacita ciyeretso ca zoipa, anakhala pa dzanja lamanja la Ukulu m'Mwamba, |
| 4 |
| atakhala wakuposa angelo, monga momwe adalowa dzina lakuposa iwo. |
| 5 |
| Pakuti kwa mngelo uti anati nthawi iri yonse, Iwe ndiwe Mwana wanga, Lero ine ndakubala Iwe? ndiponso, Ine ndidzakhala kwa iye Atate, Ndipo iye adzakhala kwa ine Mwana? |
| 6 |
| Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m'dziko, anena, Ndipo amgwadire iye angelo onse a Mulungu. |
| 7 |
| Ndipo za angelo anenadi, Amene ayesa angelo ace mizimu, Ndi omtumikira iye akhale lawi lamoto; |
| 8 |
| Koma ponena za Mwana, ati, Mpando wacifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi; Ndipo ndodo yacifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu. |
| 9 |
| Mwakonda cilungamo, ndi kudana naco coipa; Mwa ici Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani Ndi mafuta a cikondwerero ceni ceni koposa anzanu. |
| 10 |
| Ndipo, Inu, Ambuye, paciyambipo munaika maziko ace a dziko, Ndipo miyamba iri nchito ya manja anu; |
| 11 |
| Iyo idzatayika; komatu mukhalitsa; Ndipo iyo yonse idzasuka mongamaraya; |
| 12 |
| Ndi monga copfunda mudzaipinda Monga maraya, ndipo idzasanduka; Koma Inu ndinu yemweyo, Ndipo zaka zanu sizidzatha. |
| 13 |
| Koma za mngelo uti anati nthawi iri yonse, Khala pa dzanja lamanja langa, Kufikira ndikaika adani ako mpando wa ku mapazi ako? |
| 14 |
| Kodi siiri yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa cipulumutso? |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/hebrews/001.mp3
13
1