Adonizedeki mfumu ya ku Yerusalemu adamva kuti Yoswa wagonjetsa kotheratu mzinda wa Ai, ndipo waononga mzindawo pamodzi ndi mfumu yake, monga momwe adachitira Yeriko pamodzi ndi mfumu yake yomwe. Adamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni adapangana za mtendere ndi Aisraele, ndipo kuti anali kukhala pakati pao.
Motero Adonizedeki adatuma mithenga kwa Hohamu mfumu ya ku Hebroni, kwa Piramu mfumu ya ku Yaramuti, kwa Yafiya mfumu ya ku Lakisi ndi kwa Debiri mfumu ya ku Egiloni. Adatuma mau akuti,
Mafumu asanu a Aamoriwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi ndiponso ya ku Egiloni, adagwirizana. Adasonkhanitsa ankhondo ao nazinga mzinda wa Gibiyoni, ndi kuuthira nkhondo.
Anthu a ku Gibiyoni adatumiza mau kwa Yoswa ku zithando ku Giligala kuja kuti, “Mbuyathu, musatitaye ife atumiki anu. Bwerani msanga mudzatithandize! Tipulumutseni! Mafumu onse a Aamori atsika mapiri kudzamenyana nafe.”
Ndipo Chauta adauza Yoswa kuti, “Usaŵaope anthu amenewo. Ndaŵapereka kale kwa iwe kuti uŵagonjetse. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene adzatha kulimbika.”
Chauta adaŵachititsa mantha adaniwo pamene adangoona nkhondo ya Aisraele ija. Motero Aisraele adapambana Aamori ku Gibiyoni, naŵathamangitsa kutsika phiri la ku Betehoroni ndi kuŵakantha mpaka ku Azeka ndi ku Makeda.
Pamene ankathaŵa nkhondo ya Aisraeleyo kutsika phiri ku Betehoroni mpaka ku Azeka, Chauta adagwetsa miyala yaikulu yamatalala pa iwo kuchokera kumwamba, ndipo idaŵapha. Ophedwa ndi matalala anali ambiri kupambana ophedwa ndi Aisraele.
Pa tsiku limene Chauta adapatsa Aisraele mphamvu kuti agonjetse Aamori, Yoswa adalankhula naye. Tsono pamaso pa Aisraele onse adati, “Iwe dzuŵa, ima pamwamba pa Gibiyoni, iwe mwezi, ima pamwamba pa chigwa cha Ayaloni.”
Tsiku lomwelo Yoswa adathira nkhondo mzinda wa Makeda naugwira pamodzi ndi mfumu yake. Adapha onse amumzindamo, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe wotsala wamoyo. Mfumu ya ku Makeda adaichita zomwe adaichita mfumu ya ku Yeriko.
Ndipo Chauta adapereka mzindawo m'manja mwa Aisraele. Adakantha munthu aliyense mumzindamo ndi lupanga, osasiyapo ndi mmodzi yemwe. Mfumu ya mzindawo adaichita zomwe adaichita mfumu ya ku Yeriko.
Chauta adapatsa Aisraele mphamvu zogonjetsera mzinda wa Lakisi pa tsiku lachiŵiri la nkhondoyo. Tsono monga momwe adachitira ku Libina, sadapulumutsepo ndi mmodzi yemwe, koma adapha onse.
Pamenepo Horamu, mfumu ya ku Gezere, anadza kudzathandiza Lakisi, koma Yoswa adamgonjetsa pamodzi ndi anthu ake omwe, osasiyapo wamoyo ndi mmodzi yemwe.
Adaugonjetsa naulanda pamodzi ndi mfumu yake, kudzanso midzi yoyandikana nawo. Adapha anthu onse akumeneko. Yoswa adauchita mzinda wa Debiri zomwe adauchita mzinda wa Hebroni ndi Libina pamodzi ndi mafumu ake.
Yoswa adagonjetsa adani onse kuyambira ku Kadesi-Baranea chakumwera, mpaka ku Gaza kufupi ndi nyanja, kuphatikizapo dziko lonse la Goseni mpaka ku Gibiyoni.