Ndipo kunali, pamene Yabini mfumu ya ku Hazoro anacimva, anatwna kwa Yabobu mfumu ya ku Madoni, ndi kwa mfumu ya ku Simironi, ndi kwa mfumu ya ku Akasafu,
Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope cifukwa ca iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israyeli; uziwadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agareta ao ndi moto.
Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israyeli, ndipo anawakantha, nawapitikitsa mpaka ku Zidoni waukulu, ndi ku MiseripotuMaimu, ndi ku cigwa ca Mizepe kum'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyira ndi mmodzi yense.
Ndipo Yoswa analanda midzi yonse ya mafumu awa, ndi mafumu ao omwe nawakantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse; monga Mose mtumiki wa Yehova adalamulira.
Ndi zofunkha zonse za midzi iyi ndi ng'ombe ana a Israyeli anadzifunkhira; koma anakantha ndi lupanga lakuthwa anthu onse mpaka adawaononga osasiyapo ndi mmodzi yense wopuma mpweya.
Motero Yoswa analanda dziko lonselo, la kumapiri, ndi la kumwera, ndi dziko lonse la Goseni, ndi dziko la kucidikha, ndi la kucigwa; ndi la kwnapiri la Israyeli, ndi la ku cidikha cace;
kuyambira phiri la Halaki lokwera kumka ku Seiri, mpaka Baala-gadi m'cigwa ca Lebano patsinde pa phiri la Herimoni; nagwira mafwnu ao onse, nawakantha, nawapha.
Pakuti cidadzera kwa Yehova kulimbitsa mitima yao kuti athirane nao Aisrayeli nkhondo kuti iye awaononge konse, kuti asawacitire cifundo koma awaononge, monga Yehova adalamulira Mose.
Ndipo Yoswa anadza nthawi yomweyo, napasula Aanaki kuwacotsa kumapiri, ku Hebroni, ku Dibiri, ku Anabi, ndi ku mapiri onse a Yuda, ndi ku mapiri onse a Israyeli; Yoswa anawaononga konse, ndi midzi yao yomwe.