Tsono Yoswa adasonkhanitsa mafuko onse a Aisraele ku Sekemu. Adaitana akuluakulu, atsogoleri, aweruzi ndi akapitao a Aisraele, ndipo onsewo adafika pamaso pa Mulungu.
Adauza anthu onsewo kuti, “Zimene Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena ndi izi, akuti, ‘Kale makolo anu ankakhala pa mbali ina ya mtsinje wa Yufurate, ndi kumapembedza milungu ina. Mmodzi mwa makolo ameneŵa anali Tera, bambo wa Abrahamu ndi Nahori.
ndipo Isakiyo ndidampatsa Yakobe ndi Esau. Dziko lamapiri la Seiri ndidapatsa Esau kuti likhale choloŵa chake, koma Yakobe ndi ana ake adatsikira ku Ejipito.
Nditatulutsa makolo anu ku dziko la Ejipito, ndidafika nawo ku Nyanja Yofiira, koma Aejipito okwera pa magaleta ndi pa akavalo adaŵatsatira mpaka kunyanjako.
Makolo anuwo atapemphera mokhulupirira kwa Ine, ndidaika mtambo wakuda pakati pa iwo ndi Aejipitowo, ndipo nyanja idaŵamiza Aejipito onsewo. Mudapenya ndi maso anu zomwe ndidachita Ejipito, ndipo mudakhala nthaŵi yaitali m'chipululu.
“ ‘Pambuyo pake Ine ndidakufikitsani ku dziko la Aamori, amene ankakhala kuvuma kwa mtsinje wa Yordani. Adalimbana nanu iwowo, koma Ine ndidaŵapereka m'manja mwanu, mwakuti mudalanda dziko lao, chifukwa Ine ndidaŵaononga inu mukufika.
Mudaoloka Yordani ndi kufika ku Yeriko. Anthu a ku Yeriko adalimbana nanu, kudzanso Aamori, Aperizi, Akanani, Ahiti, Agirigasi, Ahivi ndi Ayebusi. Ine ndidaŵapereka m'manja mwanu.
“Tsono inu, opani Chauta ndipo mumtumikire moona ndi mokhulupirika. Chotsani milungu imene makolo anu ankaipembedza pambali pa mtsinje wa Yufurate ndi ku Ejipito, ndipo mutumikire Chauta.
Ngati simufuna kutumikira Chauta, sankhani lero lomwe lino amene muti mudzamtumikire, kapena ndi milungu ya Aamori amene mukukhala nawo m'dziko mwao. Koma ine pamodzi ndi banja langa lonse, tidzatumikira Chauta.”
Chauta, Mulungu wathu, ndiye amene adatulutsa makolo athu pamodzi ndi ife tomwe mu ukapolo, ku dziko la Ejipito. Ndipo tidaonanso ndi maso athu zinthu zazikulu zimene adachita.
Yoswayo adalemba malamulo ameneŵa m'buku la malamulo a Mulungu, ndipo adatenga chimwala chachikulu nachiimiritsa patsinde pa mtengo wa thundu pa malo opatulika a Chauta.
Aisraele adatumikira Chauta pa nthaŵi yonse ya moyo wa Yoswa ndiponso pa nthaŵi ya atsogoleri amene adakhala ndi moyo Yoswa atafa. Atsogoleriwo adadziŵa ntchito zonse zimene Chauta adachitira Israele.
Mafupa a Yosefe amene Aisraele adaŵatenga ku Ejipito, adakaŵaika ku Sekemu m'kadziko kamene Yakobe adaagula kwa ana a Hamori, bambo wa Sekemu, pa mtengo wa ndalama zasiliva zana limodzi. Ndipo dzikolo lidasanduka choloŵa cha zidzukulu za Yosefe.