Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Taonani, cikondico Atate watipatsa, kuti tichedwe ana a Mulungu; ndipo tiri ife otere. Mwa ici dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira iye. |
| 2 |
| Okondedwa, tsopano riri ana a Mulungu, ndipo sicinaoneke cimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka iye, tidzakhala ofanana ndi iye, Pakuti tidzamuona iye monga ali. |
| 3 |
| Ndipo yense wakukhala naco ciyembekezo ici pa iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera. |
| 4 |
| Yense wakucita cimo acitanso kusayeruzika; ndipo cimo ndilo kusayeruzika. |
| 5 |
| Ndipo mudziwa kuti iyeyu anaonekera kudzacotsa macimo; ndipo mwa Iye mulibe cimo. |
| 6 |
| Yense wakukhala mwa iye sacimwa; yense wakucimwa sanamuona iye, ndipo sanamdziwa iye. |
| 7 |
| Tiana, munthu asasokeretse inu; iye wakucita colungama af wolungama, monga Iyeyu ali wolungama: |
| 8 |
| iye wocita cimo ali wocokera mwa mdierekezi, cifukwa mdierekezi amacimwa kuyambira paciyambi. Kukacita ici Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge nchito za mdierekezi, |
| 9 |
| Yense wobadwa kucokera mwa Mulungu sacita cimo, cifukwa mbeu yace ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kucimwa, popeza wabadwa kucokera mwa Mulungu. |
| 10 |
| M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosacita cilungamo siali wocokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wace. |
| 11 |
| Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira paciyambi, kuti tikondane wina ndi mnzace: |
| 12 |
| osati monga Kaini anali wocokera mwa woipayo, namupha mbale wace. Ndipo anamupha iye cifukwa ninji? Popeza nchiro zace zinali zoipa, ndi za mbaie wace zolungama. |
| 13 |
| Musazizwe, abale, Jikadana nanu dziko lapansi. |
| 14 |
| Ife tidziwa kuti tacokera kuturuka muimfa kulowa m'moyo, cifukwa tikondana ndi abale iye amene sakonda akhala muimfa. |
| 15 |
| Yense wakudana ndi mbale wace ali wakupha munthu; ndipo mudziwa kun wakupha munthu ali yense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye. |
| 16 |
| Umo tizindikira cikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wace cifukwa ca ife; ndipo ife tiyener kupereka moyo wathu cifukwa ca abale. |
| 17 |
| Koma iye amene ali naco coma ca dziko lapansi, naona mbale wace ali wosowa ndi kutsekereza cifundo cace pommana iye, nanga cikondi ca Mulungu cikhala mwa iye bwanji? |
| 18 |
| Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kucita ndi m'coonadi. |
| 19 |
| Umo tidzazindikira kuti tiri ocokera m'coonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pace, |
| 20 |
| 1 m'mene monse mtima wathu utitsutsa; cifukwa Mulungu ali wamkuru woposa mitima yathu, nazindikira zonse. |
| 21 |
| Okondedwa, 2 mtima wathu ukapanda kuritsutsa, tiri nako kulimbika mtima mwa Mulungu; |
| 22 |
| ndipo 3 cimene ciri conse tipempha, tilandira kwa iye, cifukwa tisunga malamulo ace, ndipo ticita zomkondweretsa pamaso pace. |
| 23 |
| Ndipo 4 Lamulo lace ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wace Yesu Kristu, ndi 5 kukondana wina ndi mnzace, monga anatilamulira. |
| 24 |
| Ndipo 6 munthu amene asunga malamulo ace akhala mwa iye, ndi iye mwa munthuyo. Ndipo 7 m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kucokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/1john/003.mp3
5
3