Buku Loyera
|
| 1 |
| Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse. |
| 2 |
| Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: aliyense wovomereza kuti Yesu Khristu adadzakhaladi munthu, ameneyo ndi wochokera kwa Mulungu. |
| 3 |
| Koma aliyense wosavomereza Yesu, ameneyo ndi wosachokera kwa Mulungu. Maganizo akewo ndi ochokera kwa Woukira Khristu, yemwe uja mudamva kuti akubwerayu; ndipotu wafika kale m'dziko lapansi. |
| 4 |
| Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano. |
| 5 |
| Aneneri onamawo ndi apansipano, nchifukwa chake zimene amalankhula nzapansipano, ndipo anthu odalira zapansipano amaŵamvera. |
| 6 |
| Koma ife ndife ake a Mulungu. Munthu wodziŵa Mulungu, amatimvera. Koma iye amene sali wake wa Mulungu, satimvera. Umu ndi m'mene timasiyanitsira pakati pa maganizo oona ndi maganizo onama. |
| 7 |
| Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu. |
| 8 |
| Koma munthu wopanda chikondi sadziŵa Mulungu, pakuti Mulungu ndiye chikondi chimene. |
| 9 |
| Mulungu adaonetsa chikondi chake kwa ife motere: Iye nkukhala ndi Mwana mmodzi yekha, koma adamtuma pansi pano, kuti mwa Iye tikhale ndi moyo. |
| 10 |
| Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu. |
| 11 |
| Inu okondedwa, ngati Mulungu adatikonda kwambiri chotere, ifenso tiyenera kumakondana. |
| 12 |
| Palibe munthu amene adaona Mulungu. Koma tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife. |
| 13 |
| Tikudziŵa kuti timakhala mwa Mulungu, ndipo Iyenso amakhala mwa ife, chifukwa adatipatsa Mzimu wake Woyera. |
| 14 |
| Ife taona, ndipo tikuchita umboni, kuti Atate adatuma Mwana wake kuti adzakhale Mpulumutsi wa anthu a pa dziko lonse lapansi. |
| 15 |
| Aliyense wovomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye, ndipo iye amakhala mwa Mulungu. |
| 16 |
| Motero ife timadziŵa ndipo timakhulupirira ndithu kuti Mulungu amatikonda. Mulungu ndiye chikondi, ndipo munthu wokhala ndi moyo wachikondi, amakhala mwa Mulungu, Mulungunso amakhala mwa iye. |
| 17 |
| Pamene chikondi chafikira pake penipeni mwa ife ndi apa pakuti moyo wathu pansi pano uli wonga moyo wa Khristu, kotero kuti tingathe kukhala olimba mtima pa tsiku la chiweruzo. |
| 18 |
| Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye. |
| 19 |
| Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye adayamba kutikonda. |
| 20 |
| Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone. |
| 21 |
| Lamulo limene Iye adatipatsa ndi lakuti, wokonda Mulungu azikondanso mbale wake. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/1john/004.mp3
5
4