Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Kristu wabadwa kucokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wocokera mwa iye. |
| 2 |
| Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kucita malamulo ace. |
| 3 |
| Pakuti ici ndi cikondi ca Mulungu, kuti tisunge malamulo ace: ndipo malamulo ace sali olemetsa. |
| 4 |
| Pakuti ciri conse cabadwa mwa Mulungu cililaka dziko lapansi; ndipo ici ndi cilako tililaka naco dziko lapansi, ndico cikhulupiriro cathu. |
| 5 |
| Koma ndani iye wolilaka dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu |
| 6 |
| iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi; ndiye Yesu Kristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. |
| 7 |
| Ndipo Mzimu ndiye wakucita umboni, cifukwa Mzimu ndiye coonadi, |
| 8 |
| Pakuti pali atatu akucita umboni, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi. |
| 9 |
| Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uposa; cifukwa umboni wa Mulungu ndi uwu, kuti anacita umboni za Mwana wace. |
| 10 |
| Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; ye wosakhulupirira Mulungu ananuyesa iye wonama; cifukwa sanakhulupirira umboni wa Mulungu anaucita wa Mwana wace. |
| 11 |
| Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wace. |
| 12 |
| Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo. |
| 13 |
| Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu. |
| 14 |
| Ndipo uku ndi kulimbika mrima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa cifuniro cace, atimvera; |
| 15 |
| ndipo ngati tidziwa kuti atimvera ciri conse ticipempha, tidziwa kuti tiri nazo izi tazipempha kwa iye. |
| 16 |
| Wina akaona mbale wace alikucimwa cimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo iye adzampatsira moyo wa iwo akucita macimo osati a kuimfa. Pali cimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere. |
| 17 |
| Cosalungama ciri conse ciri ucimo; ndipo pali cimo losati la kuimfa. |
| 18 |
| Tidziwa kuti yense wobadwa kucokera mwa Mulungu sacimwa, koma iye wobadwa kucokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza. |
| 19 |
| Tidziwa kuti tiri ife ocokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo. |
| 20 |
| Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife cidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tiri mwa Woonayo, mwa Mwana wace Yesu Kristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha. |
| 21 |
| Tiana, 1 dzisungireni nokha kupewa mafano. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/1john/005.mp3
5
5