Pambuyo pake ndidaona buku m'dzanja lamanja la wokhala pa mpando wachifumu uja. Bukulo linali lolembedwa m'kati ndi kumbuyo komwe, ndipo linali lomatidwa ndi zimatiro zisanu ndi ziŵiri.
Apo mmodzi mwa Akuluakulu aja adandiwuza kuti, “Usalire, pakuti Mkango wa m'fuko la Yuda, chidzukulu cha mfumu Davide, wapambana, ndipo Iye angathe kufutukula bukulo ndi kumatula zimatiro zake zisanu ndi ziŵiri zija.”
Pamene adalilandira, Zamoyo zinai zija, pamodzi ndi Akuluakulu 24 aja, zidagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosayo. Aliyense mwa Akuluakuluwo anali ndi zeze ndiponso mikhate yagolide yodzaza ndi lubani. Lubaniyo ndi mapemphero a anthu a Mulungu.
Ankaimbira Mwanawankhosa uja nyimbo yatsopano iyi yakuti: “Ndinu oyenera kulandira bukuli ndi kumatula zimatiro zake. Pakuti mudaaphedwa, ndipo ndi imfa yanu mudaombolera Mulungu anthu a fuko lililonse, a chilankhulo chilichonse, ndi a mtundu uliwonse.
Ndidamvanso mau a cholengedwa chilichonse chakuthambo, cha pa dziko lapansi, cha kunsi kwa dziko, ndiponso cham'nyanja. Zolengedwa zonsezo zinkaimba mau akuti, “Wokhala pa mpando wachifumu uja, ndiponso Mwanawankhosa, alandire chiyamiko, ulemu, ulemerero ndi nyonga mpaka muyaya.”