Giliyadi analinso ndi mkazi amene anali ndi ana. Tsono ana amenewo atakula, adampirikitsa Yefita namuuza kuti, “Sudzalandirako choloŵa m'nyumba ya bambo wathu, pakuti ndiwe mwana wa kwa mkazi wina.”
Koma Yefita adaŵafunsa akuluakulu a ku Giliyadiwo kuti, “Kodi suja inu mudadana nane nkundipirikitsa ku nyumba ya bambo wanga? Chifukwa chiyani tsopano mwabwera kwa ine poona kuti muli m'mavuto?”
Apo akuluakuluwo adamuyankha Yefita kuti, “Nchimene tabwerera kwa iwe tsopano lino, kuti upite nafe kukamenyana ndi Aamoni, ndipo ukhale mtsogoleri wathu wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.”
Choncho Yefita adapita nawo akuluakulu a ku Giliyadiwo, ndipo anthu akumeneko adamsandutsa mfumu ndi mtsogoleri wao woŵalamulira. Tsono Yefita adabwerezanso kulankhula mau ake omwe aja pamaso pa Chauta ku Mizipa.
Mfumu ya Aamoniyo idaŵayankha amithenga a Yefita kuti, “Chifukwa chakuti Aisraele, pochoka ku Ejipito, adalanda dziko langa kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki mpakanso ku mtsinje wa Yordani. Tsono mundibwezere dziko mwamtendere.”
Nthaŵi imeneyo Aisraele adatuma amithenga kwa mfumu ya ku Edomu kukaiwuza kuti, ‘Tapota nanu, mutilole kuti tidzere m'dziko mwanu.’ Koma mfumu ya ku Edomuyo sidafune kumva zimenezo. Adatumanso amithenga ena kwa mfumu ya ku Mowabu, koma nayonso sidavomereze zimenezo. Choncho Aisraele adakhala ku Kedesi.
Pambuyo pake adanyamuka ulendo wao kudzera ku chipululu nazungulira dziko la Edomu ndi dziko la Mowabu, ndipo adafika kuvuma kwa Arinoni. Koma sadaloŵe m'dziko la Mowabu, pakuti mtsinje wa Arinoni unali malire a dziko la Mowabu.
Koma Chauta, Mulungu wa Aisraele, adampereka Sihoniyo pamodzi ndi anthu ake onse m'manja mwa Aisraele naŵagonjetsa. Choncho Aisraele adalanda chigawo chonse cha dziko la Aamori amene ankakhala m'dzikolo.
Adalanda chigawo chonse cha dziko la Aamori kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki, ndipo kuyambira ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yordani.
Pa zaka mazana atatu Aisraele ankakhala ku Hesiboni ndi m'milaga yake, ku Aroere ndi m'milaga yake, ndiponso m'mizinda yonse imene ili m'mbali mwa mtsinje wa Arinoni, nanga chifukwa chiyani simunkalanda malowo nthaŵi imeneyo?
Tsono Mzimu wa Chauta udatsikira Yefita, ndipo iye adanyamuka nadzera ku Giliyadi ndi ku Manase. Adakafika ku Mizipa, mzinda wa Giliyadi, ndipo kuchokera ku Mizipako adakafika kumbuyo kwa Aamoni.
Adaŵakanthadi kuyambira ku Aroere mpaka pafupi ndi mzinda wa Miniti, mizinda makumi aŵiri pamodzi, ndiponso mpaka ku Abele-Keranimu. Motero Aamoni adagonjetsedwa ndi Aisraele.