Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Pamenepo amuna a Efuremu analalikidwa, napita kumpoto; nati kwa Yefita, Wapitiriranji kuthira nkhondo ana a Amoni, osatiitana ife timuke nawe? Tidzakutenthera nyumba yako ndi moto pamtu pako. |
| 2 |
| Ndipo Yefita anati kwa iwo, Ine ndi anthu anga tinatsutsana kwakukulu ndi ana a Amoni, koma pamene ndinakuitanani inu simunandipulumutsa m'dzanja lao. |
| 3 |
| Ndipo pakuona ine kuti simundipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundichitira nkhondo? |
| 4 |
| Pamenepo Yefita anamemeza amuna onse a m'Giliyadi nalimbana naye Efuremu; ndipo amuna a Giliyadi anakantha Efuremu, chifukwa adati, Inu Agiliyadi ndinu akuthawa Efuremu, pakati pa Efuremu ndi pakati pa Manase. |
| 5 |
| Ndipo Agiliyadi anatsekereza madooko a Yordani a Efuremu; ndipo kunatero kuti, akati othawa a Efuremu, Ndioloke, amuna a Giliyadi anati kwa Iye, Ndiwe Mwefuremu kodi? Akati, Iai; |
| 6 |
| pamenepo anati kwa iye, Unene tsono Shiboleti; ndipo akati, Siboleti, osakhoza kutchula bwino, amgwira namupha padooko pomwe pa Yordani; ndipo anagwa a Efuremu nthawi ija, zikwi makumi anai mphambu ziwiri. |
| 7 |
| Ndipo Yefita anaweruza Israele zaka zisanu ndi chimodzi; nafa Yefita Mgiliyadi, naikidwa m'mudzi wina wa Giliyadi. |
| 8 |
| Ndi pambuyo pake Ibizani wa ku Betelehemu anaweruza Israele. |
| 9 |
| Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu; ndi ana akazi makumi atatu anawakwatitsa kwina, natengera ana ake amuna ana akazi makumi atatu ochokera kwina. Ndipo anaweruza Israele zaka zisanu ndi ziwiri. |
| 10 |
| Nafa Ibizani naikidwa ku Betelehemu. |
| 11 |
| Ndi pambuyo pake Eloni Mzebuloni anaweruza Israele; naweruza Israele zaka khumi. |
| 12 |
| Nafa Eloni Mzebuloni naikidwa m'Ayaloni m'dziko la Zebuloni. |
| 13 |
| Ndi pambuyo pake Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni anaweruza Israele. |
| 14 |
| Ndipo anali nao ana amuna makumi anai ndi zidzukulu zazimuna makumi atatu, akuyenda okwera pa ana a abulu makumi asanu ndi awiri; naweruza Israele zaka zisanu ndi zitatu. |
| 15 |
| Nafa Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni, naikidwa m'Piratoni m'dziko la Efuremu ku mapiri a Amaleke. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/judges/012.mp3
21
12