Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kucokera ku Giligala kumka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kucokera ku Aigupto, ndi kulowetsa inu m'dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyola cipangano canga nanu ku nthawi yonse; |
| 2 |
| ndipo inu, musamacita pangano ndi nzika za m'dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvera mau anga; mwacicita ici cifukwa ninji? |
| 3 |
| Cifukwa cacenso ndinati, Sindidzawapitikitsa kuwacotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m'nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha. |
| 4 |
| Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israyeli, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi. |
| 5 |
| Potero analicha dzina la malowo Bokimu: namphera Yehova nsembe pomwepo. |
| 6 |
| Pamene Yoswa atawalola anthu amuke, ana a Israyeli anamuka, yense ku colowa cace, dziko likhale lao lao. |
| 7 |
| Ndipo anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa ndi masiku onse a akulu akulu otsala atafa Yoswa, amene adaona nchito yaikuru yonse ya Yehova anaicitira Israyeli. |
| 8 |
| Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova anafa wa zaka zace zana ndi khumi. |
| 9 |
| Ndipo anamuika m'malire a colowa cace m'Timinatiheresi, ku mapiri a Efraimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi. |
| 10 |
| Ndiponso mbadwo uwu wonse unasonkhanidwa kuikidwa kwa makolo ao; nuuka mbadwo wina pambuyo pao; wosadziwa Yehova kapena nchitoyi adaicitira Israyeli, |
| 11 |
| Ndipo ana a Israyeli anacita coipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala; |
| 12 |
| nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawaturutsa m'dziko la Aigupto, natsata milungu yina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova. |
| 13 |
| Ndipo anasiya Yehova, natumikira Baala ndi Asitaroti. |
| 14 |
| Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao. |
| 15 |
| Kuli konse anaturuka, dzanja la Yehova linawakhalira moipa, monga Yehova adanena, ndi monga Yehova adawalumbirira; nasautsika kwambiri iwowa. |
| 16 |
| Ndipo Yehova anautsa oweruza, amene anawapulumutsa m'dzanja la iwo akuwafunkha. |
| 17 |
| Koma sanamvera angakhale oweruza ao, pakuti anamuka kupembedza milungu yina, naigwadira; anapambuka msanga m'njira yoyendamo makolo ao, pomvera malamulo a Yehova; sanatero iwowa. |
| 18 |
| Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m'dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa cisoni pa kubuula kwao cifukwa ca iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza. |
| 19 |
| Koma kunali atafa woweruzayo anabwerera m'mbuyo, naposa makolo ao ndi kucita moipitsa, ndi kutsata milungu yina kuitumikira ndi kuigwadira, sanaleka kanthu ka macitidwe ao kapena ka njira yao yacheni. |
| 20 |
| Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli; nati Iye, Popezamtundu uwu unalakwira cipangano canga cunene ndinalamulira makolo ao, osamvera mau ansa; |
| 21 |
| lnenso sindionjeza kuingitsa pamaso pao a mitundu yina imene Yoswa adaisiya pakufa iyeyu; |
| 22 |
| kuti ndiyese nayo Israyeli ngati adzasunga njira ya Yehova kuyendamo monga anaisunga makolo ao, kapena iai. |
| 23 |
| Motero Yehova analeka mitundu iyi osaiingitsa msanga, ndipo sadaipereka m'dzanja la yoswa. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/judges/002.mp3
21
2