Nati ana a Israyeli, Ndani iye mwa mapfuko onse a Israyeli amene sanakwera kudza kumsonkhano kwa Yehova? pakuti panali lumbiro lalikuru pa iye wosakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa, ndi kuti, Aphedwe ndithu.
Nati iwo, Kodi pali lina la mapfuko a Israyeli losakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa? Ndipo taonani, kucokera ku Yabesi-gileadi sanadza mmodzi kumisasa, kumsonkhano.
Ndipo msonkhano unatumizako amuna zikwi khumi ndi ziwiri, ndiwo ngwazi, nawalamulira ndi kuti, Mukani, nimuwakanthe okhala m'Yabesi-gileadi ndi lupanga lakuthwa, ndi akazi ndi ana ang'ono.
Natiiwo, Taonani, pali madyerero a Yehova caka ndi caka ku Silo, ndiko kumpoto kwa Beteli, kum'mawa kwa mseu wokwera kucokera ku Beteli kumka ku Sekemu, ndi kumwela kwa Lebona.
nimuyang'ane, ndipo taonani, ataturuka ana akazi a Silo kubvinabvina, pamenepo muturuke m'minda yamphesa ndi kudzigwirira yense mkazi wace mwa ana akazi a Silo, ndi kumuka naye ku dziko la Benjamini.