Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo iyo ndiyo mitundu ya anthu anaisiyapo Yehova kuyesa nayo Israele, ndiwo onse amene sanadziwe nkhondo zonse za Kanani; |
| 2 |
| chifukwa chake ndicho chokha chakuti adziwitse mibadwo ya ana a Israele ndi kuwaphunzitsa nkhondo, ngakhale iwo okhaokha osaidziwa konse kale; |
| 3 |
| anasiya mafumu asanu a Afilisti ndi Akanani onse, ndi Asidoni, ndi Ahivi okhala m'phiri la Lebanoni, kuyambira phiri la Baala-Heremoni mpaka polowera ku Hamati. |
| 4 |
| Amenewo anakhala choyesera Israele kuti Yehova adziwe ngati adzamvere malamulo ake, amene analamulira makolo ao mwa dzanja la Mose. |
| 5 |
| Ndipo ana a Israele anakhala pakati pa Akanani, Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi; |
| 6 |
| nakwatira ana akazi a iwowa, napereka ana ao akazi kwa ana amuna a iwowa natumikira milungu yao. |
| 7 |
| Ndipo ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova, naiwala Yehova Mulungu wao, natumikira Abaala ndi zifanizo. |
| 8 |
| Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele ndipo anawagulitsa m'dzanja la Kusani-Risataimu, mfumu ya Mesopotamiya; ndi ana a Israele anatumikira Kusani-Risataimu zaka zisanu ndi zitatu. |
| 9 |
| Ndipo pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anaukitsira ana a Israele mpulumutsi amene anawapulumutsa, ndiye Otiniyele mwana wa Kenazi, mng'ono wake wa Kalebe. |
| 10 |
| Ndipo unamdzera mzimu wa Yehova, iye naweruza Israele, natuluka kunkhondo; napereka Yehova Kusani-Risataimu mfumu ya Mesopotamiya m'dzanja lake; ndi dzanja lake linamlaka Kusani-Risataimu. |
| 11 |
| Pamenepo dziko linapumula zaka makumi anai; ndi Otiniyele mwana wa Kenazi anafa. |
| 12 |
| Koma ana a Israele anaonjezanso kuchita choipa pamaso pa Yehova; pamenepo Yehova analimbitsa Egiloni mfumu ya Mowabu pa Israele, popeza anachita choipa pamaso pa Yehova. |
| 13 |
| Ndipo anadzisonkhanitsira ana a Amoni ndi a Amaleke, namuka nakantha Israele, nalanda mudzi wa m'migwalangwa nakhalamo. |
| 14 |
| Ndipo ana a Israele anatumikira Egiloni mfumu ya Mowabu zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu. |
| 15 |
| Koma pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anawaukitsira mpulumutsi, Ehudi mwana wa Gera, Mbenjamini, munthu wamanzere, ndipo ana a Israele anatumiza mtulo m'dzanja lake kwa Egiloni mfumu ya Mowabu. |
| 16 |
| Ndipo Ehudi anadzisulira lupanga lakuthwa konsekonse utali wake mkono; nalimangirira pansi pa zovala zake pa ntchafu ya kulamanja. |
| 17 |
| Ndipo anapereka mtulo kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu; koma Egiloni ndiye munthu wonenepa ndithu. |
| 18 |
| Ndipo atatha kupereka mtulowo, anauza anthu onyamula mtulo achoke. |
| 19 |
| Koma iye mwini anabwerera pa mafano osema ali ku Giligala, nati, Ndili nao mau achinsinsi kwa inu, mfumu. Nati iye, Khalani chete. Ndipo anatuluka onse akuimapo. |
| 20 |
| Ndipo Ehudi anamdzera alikukhala pa yekha m'chipinda chosanja chopitidwa mphepo. Nati Ehudi, Ndili nao mau a Mulungu akukuuzani. Nauka iye pa mpando wake. |
| 21 |
| Ndipo Ehudi anatulutsa dzanja lake lamanzere nagwira lupanga ku ntchafu ya kulamanja nampyoza m'mimba mwake; |
| 22 |
| ndi chigumbu chake chinalowa kutsata mpeni wake; ndi mafuta anaphimba mpeniwo, pakuti sanasolole lupanga m'mimba mwake; nilituluka kumbuyo. |
| 23 |
| Pamenepo Ehudi anatuluka kukhonde namtsekera pamakomo pa chipinda chosanja nafungulira. |
| 24 |
| Ndipo atatuluka iye, anadza akapolo ake; napenya, ndipo taonani pamakomo pa chipinda chosanja mpofungulira; nati iwo, Angophimba mapazi m'chipinda chake chosanja chopitidwa mphepo. |
| 25 |
| Ndipo analindirira mpaka anachita manyazi; koma taonani, sanatsegule pamakomo pa chipinda chosanja. Pamenepo anatenga mfungulo natsegula; ndipo taonani, mbuye wao wagwa pansi, wafa. |
| 26 |
| Ndipo Ehudi anapulumuka pakuchedwa iwo, napitirira pa mafano osema, napulumuka kufikira Seira. |
| 27 |
| Ndipo kunali, pakufika iye anaomba lipenga ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anatsika naye kuchokera kumapiri, nawatsogolera iye. |
| 28 |
| Ndipo ananena nao, Nditsateni ine, pakuti Yehova wapereka adani anu Amowabu m'manja mwanu. Ndipo anatsika ndi kumtsata, natsekereza Amowabu madooko a Yordani, osalola mmodzi aoloke. |
| 29 |
| Ndipo anakantha Amowabu nyengo ija anthu zikwi khumi, onsewa anthu amoyo, ndi ngwazi; ndipo sanapulumuke ndi mmodzi yense. |
| 30 |
| Motero anagonjetsa Mowabu tsiku lija pansi pa dzanja la Israele. Ndipo dziko linapumula zaka makumi asanu ndi atatu. |
| 31 |
| Atapita iye kunali Samigara, mwana wa Anati amene anakantha Afilisti mazana asanu ndi limodzi ndi mtoso wa ng'ombe; nayenso anapulumutsa Israele. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/judges/003.mp3
21
3