Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova, atafa Ehudi. |
| 2 |
| Ndipo Yehova anawagulitsa m'dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wochita ufumu ku Hazori; kazembe wake wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti wa amitundu. |
| 3 |
| Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri. |
| 4 |
| Ndipo Debora, mneneri wamkazi, ndiye mkazi wake wa Lapidoti, anaweruza Israele nyengo ija. |
| 5 |
| Ndipo anakhala patsinde pa mgwalangwa wa Debora pakati pa Rama ndi Betele ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anakwera kwa iye awaweruze. |
| 6 |
| Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinowamu, achoke m'Kedesi-Nafutali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israele sanalamulire ndi kuti, Muka, nulunjike kuphiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafutali ndi ana a Zebuloni? |
| 7 |
| Ndipo ndidzamkoka Sisera, kazembe wa nkhondo ya Yabini, akudzere ku mtsinje wa Kisoni, ndi magaleta ake, ndi aunyinji ake; ndipo ndidzampereka m'dzanja lako. |
| 8 |
| Ndipo Baraki anati kwa iye, Ukamuka nane, ndidzamuka; ukapanda kumuka nane, sindimuka. |
| 9 |
| Nati iye, Kumuka ndidzamuka nawe, koma ulendo umukawo, sudzachita nao ulemu; pakuti Yehova adzagulitsa Sisera m'dzanja la mkazi. Motero Debora anauka namuka ndi Baraki ku Kedesi. |
| 10 |
| Ndipo Baraki anaitana Zebuloni ndi Nafutali asonkhane ku Kedesi; iye nakwera ndi anthu zikwi khumi akumtsata; Deboranso anakwera kunka naye. |
| 11 |
| Ndipo Hebere Mkeni anadzisiyanitsa ndi Akeni, ndi ana a Hobabu mlamu wake wa Mose, namanga mahema ake mpaka thundu wa m'Zaananimu, ndiwo wa ku Kedesi. |
| 12 |
| Ndipo anauza Sisera kuti Baraki mwana wa Abinowamu wakwera kuphiri la Tabori. |
| 13 |
| Pamenepo Sisera anasonkhanitsa magaleta ake onse ndiwo magaleta mazana asanu ndi anai achitsulo, ndi anthu onse okhala naye, kuyambira Haroseti wa amitundu mpaka mtsinje wa Kisoni. |
| 14 |
| Ndipo Debora anati kwa Baraki, Nyamuka; pakuti ili ndi tsikuli Yehova wapereka Sisera m'dzanja lako; sanatuluke kodi Yehova pamaso pako? Potero Baraki anatsika kuphiri la Tabori ndi amuna zikwi khumi akumtsata. |
| 15 |
| Ndipo Ambuye anaononga Sisera ndi magaleta onse ndi gulu lankhondo lonse, ndi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki; koma Sisera anatsika pagaleta nathawa choyenda pansi. |
| 16 |
| Koma Baraki anatsata magaleta ndi gululo mpaka Haroseti wa amitundu; ndi gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga lakuthwa, sanatsale munthu ndi mmodzi yense. |
| 17 |
| Koma Sisera anathawira choyenda pansi ku hema wa Yaele mkazi wa Hebere Mkeni; pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori, ndi nyumba ya Hebere Mkeni. |
| 18 |
| Ndipo Yaele anatuluka kukomana ndi Sisera, nanena naye, Patuka, mbuye wanga, patukira kwa ine kuno; usaope. Ndipo anapatukira kwa iye kulowa m'hema, namfunda ndi chimbwi. |
| 19 |
| Pamenepo ananena naye, Ndipatsetu madzi pang'ono ndimwe; popeza ndine waludzu. Ndipo anatsegula thumba la mkaka, nampatsa amwe, namfunda. |
| 20 |
| Ndipo Sisera ananena naye, Taima pakhomo pa hema, ndipo kudzali, akadza munthu, akakufunsa akati, Pali munthu pano kodi? Uziti, Palibe. |
| 21 |
| Pamenepo Yaele mkazi wa Hebere anatenga chichiri cha hema, natenga nyundo m'dzanja lake namdzera monyang'ama, nakhomera chichiri chilowe m'litsipa mwake; nichinapyoza kulowa m'nthaka; popeza anali m'tulo tofa nato ndi kulema; nafa. |
| 22 |
| Ndipo taonani, pomlondola Sisera Barakiyo, Yaele anatuluka kukomana naye, nati kwa iye, Idza kuno, ndidzakuonetsa munthu umfunayo. Potero anamdzera, ndipo taonani, Sisera wagwa, wafa, ndi chichiri m'litsipa mwake. |
| 23 |
| Momwemo Mulungu anagonjetsa tsiku lija Yabini mfumu ya Kanani pamaso pa ana a Israele. |
| 24 |
| Ndipo dzanja la ana a Israele linamkabe ndi kulimbika pa Yabini mfumu ya Kanani mpaka adamuononga Yabini mfumu ya Kanani. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/judges/004.mp3
21
4