Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo Debora ndi Baraki mwana wa Abinowamu anaimba tsiku lomwelo ndi kuti, |
| 2 |
| Lemekezani Yehova pakuti atsogoleri m'Israele anatsogolera, pakuti anthu anadzipereka mwaufulu. |
| 3 |
| Imvani mafumu inu; tcherani makutu, akalonga inu; ndidzamuimbira ine Yehova, inetu; ndidzamuimbira nyimbo, Yehova, Mulungu wa Israele. |
| 4 |
| Yehova, muja mudatuluka m'Seiri, muja mudayenda kuchokera ku thengo la Edomu, dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha, inde mitambo inakha madzi. |
| 5 |
| Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova, Sinai lili pamaso pa Yehova, Mulungu wa Israele. |
| 6 |
| Masiku a Samigara, mwana wa Anati, masiku a Yaele maulendo adalekeka ndi apanjira anayenda mopazapaza. |
| 7 |
| Milaga idalekeka m'Israele, idalekeka. Mpaka ndinauka ine Debora, ndinauka ine amai wa Israele. |
| 8 |
| Anasankha milungu yatsopano, pamenepo nkhondo inaoneka kuzipata. Ngati chikopa kapena nthungo zidaoneka mwa zikwi makumi anai a Israele? |
| 9 |
| Mtima wanga uvomerezana nao olamulira a m'Israele, amene anadzipereka mwaufulu mwa anthu. Lemekezani Yehova. |
| 10 |
| Inu akuyenda okwera pa abulu oyera, inu akukhala poweruzira, ndi inu akuyenda m'njira, fotokozerani. |
| 11 |
| Posamveka phokoso la amauta potunga madzi, pomwepo adzafotokozera zolungama anazichita Yehova, zolungama anazichita m'milaga yake, m'Israele. Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata. |
| 12 |
| Galamuka, Debora, galamuka, galamuka, galamuka, unene nyimbo; uka, Baraki, manga nsinga ndende zako, mwana wa Abinowamu, iwe. |
| 13 |
| Pamenepo omveka otsala anatsika ndi anthu; Yehova ananditsikira pakati pa achamuna. |
| 14 |
| Anafika Aefuremu amene adika mizu m'Amaleke; Benjamini anakutsata iwe pakati pa anthu ako. Ku Makiri kudachokera olamulira, ndi ku Zebuloni iwo akutenga ndodo ya mtsogoleri. |
| 15 |
| Akalonga a Isakara anali ndi Debora; monga Isakara momwemo Baraki, anawatuma m'chigwa namka choyenda pansi. Pa mitsinje ya Rubeni panali zotsimikiza mtima zazikulu. |
| 16 |
| Wakhaliranji pakati pa makola, kumvera kulira kwa zoweta? Ku timitsinje ta Rubeni kunali zotsimikiza mtima zazikulu. |
| 17 |
| Giliyadi anakhala tsidya lija la Yordani; ndi Dani, akhaliranji m'zombo? Asere anakhala pansi m'mphepete mwa nyanja, nakhalitsa pa nyondo yake ya nyanja. |
| 18 |
| Zebuloni ndiwo anthu anataya moyo wao mpaka imfa, Nafutali yemwe poponyana pamisanje. |
| 19 |
| Anadza mafumu nathira nkhondo; pamenepo anathira nkhondo mafumu a Kanani. M'Taanaki, ku madzi a Megido; osatengako phindu la ndalama. |
| 20 |
| Nyenyezi zinathira nkhondo yochokera kumwamba, m'mipita mwao zinathirana ndi Sisera. |
| 21 |
| Mtsinje wa Kisoni unawakokolola, mtsinje uja wakale, mtsinje wa Kisoni. Yenda mwamphamvu, moyo wangawe. |
| 22 |
| Pamenepo ziboda za akavalo zinaguguda. Ndi kutumphatumpha, kutumphatumpha kwa anthu ake eni mphamvu. |
| 23 |
| Mutemberere Merozi, ati mthenga wa Yehova, mutemberere chitemberere nzika zake; pakuti sanadzathandize Yehova, kumthandiza Yehova pa achamuna. |
| 24 |
| Wodalitsika, woposa akazi, akhale Yaele mkazi wa Hebere Mkeni. Akhale wodalitsika woposa akazi a m'hema. |
| 25 |
| Mwamunayo anapempha madzi, anampatsa mkaka, anamtengera mafuta a mkaka m'chotengera cha mfulu. |
| 26 |
| Dzanja lake analitambasulira kuchichiri, ndi dzanja lake lamanja ku nyundo ya antchito, nakhomera Sisera, nakantha mutu wake, inde, anaphwanya napyoza m'litsipa mwake. |
| 27 |
| Pa mapazi ake anabzong'onyoka, anagwa, anagona; pa mapazi ake anabzong'onyoka, anagwa; pobzong'onyokapo, pamenepo wagwa wafa. |
| 28 |
| Anapenyerera ali pazenera, nafuula Make wa Sisera, pa sefa wake, achedweranji galeta wake? Zizengerezeranji njinga za magaleta ake? |
| 29 |
| Akazi anzake omveka anzeru anamyankha; koma anadziyankhira yekha mau. |
| 30 |
| Kodi sanapeze, sanagawe zofunkha? Namwali, anamwali awiri kwa munthu aliyense. Chofunkha cha nsalu za mawangamawanga kwa Sisera; chofunkha cha nsalu za mawangamawanga, za maluwa, nsalu za mawangamawanga, za maluwa konsekonse, kwa chofunkha cha khosi lake. |
| 31 |
| Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda Inu akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake. Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/judges/005.mp3
21
5