Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo amuna a Efuremu anati kwa iye, Ichi watichitira nchiyani, osatiitana popita iwe kulimbana ndi Amidiyani? Natsutsana naye kolimba. |
| 2 |
| Koma ananena nao, Ndachitanji tsopano monga inu? Kodi kukunkha mphesa kwa Efuremu sikuposa kutchera mphesa kwa Abiyezere? |
| 3 |
| Mulungu anapereka m'dzanja lanu akalonga a Midiyani, Orebu ndi Zeebu, ndipo ndinakhoza kuchitanji monga inu? Pamenepo mkwiyo wao unamlezera, atanena mau awa. |
| 4 |
| Ndipo Gideoni anafika ku Yordani, naoloka, iye ndi amuna mazana atatu anali naye, ali otopa koma ali chilondolere. |
| 5 |
| Ndipo ananena kwa amuna a ku Sukoti, Mupatsetu anthu awa akunditsata mitanda yamkate; pakuti atopa, ndipo ndilikulondola Zeba ndi Zalimuna mafumu a Midiyani. |
| 6 |
| Koma akalonga a ku Sukoti anati, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna ali m'dzanja lako tsopano apa, kuti ife tiwaninkhe ankhondo ako mkate? |
| 7 |
| Ndipo Gideoni anati, Chifukwa chake, Yehova akapereka Zeba ndi Zalimuna m'dzanja langa, ndidzapuntha nyama yanu ndi minga ya m'chipululu ndi mitungwi. |
| 8 |
| Ndipo anachokapo kukwera ku Penuwele, nanena nao momwemo; ndipo amuna a ku Penuwele anamyankha monga adamyankha amuna a ku Sukoti. |
| 9 |
| Ndipo ananenanso kwa amuna a ku Penuwele ndi kuti, Ndikabwerera ndi mtendere ndidzagumula nsanja iyi. |
| 10 |
| Zeba ndi Zalimuna ndipo anali m'Karikori, ndi a m'misasa ao pamodzi nao, amuna monga zikwi khumi ndi zisanu; ndiwo otsala onse a khamu lonse la ana a kum'mawa; popeza atagwa amuna zikwi zana limodzi ndi makumi awiri akusolola lupanga. |
| 11 |
| Ndipo Gideoni anakwerera njira ya iwo okhala m'mahema kum'mawa kwa Noba, ndi Yogobeha, nakantha khamulo popeza khamulo linakhala lokhazikika mtima. |
| 12 |
| Ndipo Zeba ndi Zalimuna anathawa; koma anawatsata, nagwira mafumu awiri a Midiyani Zeba ndi Zalimuna, nanjenjemeretsa khamu lonse. |
| 13 |
| Pamenepo Gideoni mwana wa Yowasi anabwerera kunkhondo pokwerera pa Heresi. |
| 14 |
| Ndipo anagwira mnyamata wa anthu a ku Sukoti, nafunsira; ndipo anamsimbira akalonga a ku Sukoti, ndi akulu ake amuna makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi awiri. |
| 15 |
| Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Zalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna akhala m'dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema? |
| 16 |
| Ndipo anagwira akulu a m'mudzi ndi minga ya kuchipululu ndi mitungwi, nawalanga nazo amuna a ku Sukoti. |
| 17 |
| Ndipo anagamula nsanja ya Penuwele, napha amuna akumudzi. |
| 18 |
| Pamenepo anati kwa Zeba ndi Zalimuna, Amunawo munawapha ku Tabori anali otani? Iwo nayankha, Monga iwe momwemo iwowa; yense wakunga mwana wa mfumu. |
| 19 |
| Ndipo anati, Ndiwo abale anga, ana a mai wanga. Pali Yehova mukadawasunga amoyo, sindikadakuphani. |
| 20 |
| Nati kwa Yetere mwana wake woyamba, Tauka, nuwaphe. Koma mnyamatayo sanasolole lupanga lake; pakuti anaopa, pokhala anali mnyamata. |
| 21 |
| Pamenepo Zeba ndi Zalimuna anati, Tauka iwe mwini nutigwere; pakuti monga munthu momwemo mphamvu yake. Ndipo Gideoni anauka nawapha Zeba ndi Zalimuna, nalanda mphande zinali kukhosi kwa ngamira zao. |
| 22 |
| Pamenepo anthu a Israele anati kwa Gideoni, Mutilamulire ndi inu, ndi mwana wanu, ndi mdzukulu wanu, pakuti mwatipulumutsa m'dzanja la Amidiyani. |
| 23 |
| Koma Gideoni ananena nao. Sindidzalamulira inu, ngakhale mwana wanga sadzalamulira inu; Yehova adzalamulira inu. |
| 24 |
| Gideoni anatinso kwa iwo, Mundilole ndipemphe kanthu kamodzi kwa inu, mundipatse aliyense maperere mwa zofunkha zanu; pakuti anali nao maperere agolide, pokhala anali Aismaele. |
| 25 |
| Ndipo anayankha, Kupereka tiwapereka; nayalapo chovala, naponyamo yense maperere a mwa zofunkha zao. |
| 26 |
| Ndipo kulemera kwake kwa maperere agolide adawapempha ndiko masekeli chikwi chimodzi ndi mazana asanu ndi awiri; osawerenga mphande, ndi zitunga ndi zovala zachibakuwa za pa mafumu a ku Midiyani, osawerenganso maunyolo okhala pa makosi a ngamira zao. |
| 27 |
| Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m'mudzi mwake, ndiwo Ofura; ndi Israele yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yake ngati msampha. |
| 28 |
| Motero anagonjetsa Amidiyani pamaso pa ana a Israele, osaweramutsanso mitu yao iwowa. Ndipo dziko lidapumula zaka makumi anai m'masiku a Gideoni. |
| 29 |
| Ndipo Yerubaala, mwana wa Yowasi anamuka, nakhala m'nyumba ya iye yekha. |
| 30 |
| Nakhala nao ana amuna makumi asanu ndi awiri Gideoni, anawabala ndi iye; popeza anali nao akazi ambiri. |
| 31 |
| Ndipo mkazi wake wamng'ono wokhala m'Sekemu, iyenso anambalira mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Abimeleki. |
| 32 |
| Ndipo Gideoni mwana wa Yowasi anafa atakalamba bwino, naikidwa m'manda a Yowasi atate wake, m'Ofura wa Aabiyezere. |
| 33 |
| Ndipo kunali, atafa Gideoni, ana a Israele anabwereranso nagwadira Abaala, nayesa Baala-Beriti mulungu wao. |
| 34 |
| Ndi ana a Israele sanakumbukire Yehova Mulungu wao, amene anawapulumutsa m'dzanja la adani ao onse pozungulira ponse; |
| 35 |
| osachitira chifundo nyumba ya Yerubaala, ndiye Gideoni, monga mwa zokoma zonse iye anachitira Israele. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/judges/008.mp3
21
8