Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Koma Abimeleki mwana wa Yerubaala anamuka ku Sekemu kwa abale a amai wake, nanena nao, ndi kwa banja lonse la nyumba ya atate wa amai wake, ndi kuti, |
| 2 |
| Nenanitu m'makutu mwa eni ake onse a ku Sekemu, Chokomera inu nchiti, akulamulireni ana amuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? Mukumbukirenso kuti ine ndine wa fuko lanu ndi nyama yanu. |
| 3 |
| Pamenepo abale a amake anamnenera mau awa onse m'makutu a eni ake onse a Sekemu; ndi mitima yao inalunjika kutsata Abimeleki; pakuti anati, Ndiye mbale wathu. |
| 4 |
| Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m'nyumba ya Baala-Beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pake ndi opepuka amene anamtsata. |
| 5 |
| Ndipo anamuka kunyumba ya atate wake ku Ofura, nawapha abale ake ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala. |
| 6 |
| Pamenepo anasonkhana eni ake onse a ku Sekemu, ndi nyumba yonse ya Milo, namuka namlonga Abimeleki ufumu pa thundu wa choimiritsa chili m'Sekemu. |
| 7 |
| Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu pa phiri la Gerizimu, nakweza mau ake, nafuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ake a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu. |
| 8 |
| Kumuka inamuka mitengo kudzidzozera mfumu; niti kwa mtengo wa azitona, Ukhale iwe mfumu yathu. |
| 9 |
| Koma mtengo wa azitona unati kwa iwo, Ngati ndidzasiya kunona kwanga kumene alemekeza nako Mulungu ndi anthu kukalenga pa mitengo? |
| 10 |
| Pamenepo mitengo inati kwa mkuyu. Tiye iwe, ukhale mfumu yathu. |
| 11 |
| Koma mkuyu unanena nao, Ngati ndidzasiya kuzuna kwanga, ndi zipatso zanga zokoma kukalenga pa mitengo? |
| 12 |
| Pamenepo mitengo inati kwa mpesa, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu. |
| 13 |
| Koma mpesa unanena nao, Ngati ndidzasiya vinyo wanga wakusekeretsa Mulungu ndi anthu, kukalenga pa mitengo? |
| 14 |
| Pamenepo mitengo yonse inati kwa nkandankhuku, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu. |
| 15 |
| Ndipo nkandankhuku unati kwa mitengo, Mukandidzoza mfumu yanu moonadi, tiyeni, thawirani ku mthunzi wanga; mukapanda kutero utuluke moto m'nkandankhuku ndi kunyeketsa mikungudza ya Lebanoni. |
| 16 |
| Ndipo tsopano, ngati mwachita moona ndi mwangwiro pakulonga Abimeleki ufumu, ngatinso mwamchitira chokoma Yerubaala ndi nyumba yake, ndi kumchitira monga anayenera manja ake; |
| 17 |
| pakuti atate wanga anakugwirirani nkhondo, nataya moyo wake, nakupulumutsani m'dzanja la Amidiyani; |
| 18 |
| koma mwaukira nyumba ya atate wanga lero lino, ndi kuwapha ana ake, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; ndipo mwalonga Abimeleki mwana wa mdzakazi wake, akhale mfumu ya pa eni ake a ku Sekemu, chifukwa ali mbale wanu; |
| 19 |
| ngati tsono mwachitira Yerubaala ndi nyumba yake zoona ndi zangwiro lero lino, kondwerani naye Abimeleki, nayenso akondwere nanu; |
| 20 |
| koma ngati simunatero, utuluke moto kwa Abimeleki, nunyeketse eni ake a ku Sekemu ndi nyumba ya Milo; nutuluke moto kwa eni ake a ku Sekemu, ndi kunyumba yake ya Milo, nunyeketse Abimeleki. |
| 21 |
| Pamenepo Yotamu anafulumira, nathawa, namuka ku Beere, nakhala komweko, chifukwa cha Abimeleki mbale wake. |
| 22 |
| Abimeleki atakhala kalonga wa Israele zaka zitatu, |
| 23 |
| Mulungu anatumiza mzimu woipa pakati pa Abimeleki ndi eni ake a ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamchitira Abimeleki mosakhulupirika; |
| 24 |
| kuti chiwawa adachitira ana amuna makumi asanu ndi awiri a Yerubaala chimdzere, ndi kuti mwazi wao uikidwe pa mbale wao Abimeleki anawaphayo, ndi pa eni ake a ku Sekemu, amene analimbikitsa manja ake, awaphe abale ake. |
| 25 |
| Ndipo eni ake a ku Sekemu anaika omlalira pamwamba pa mapiri; amene anawawanya onse akudzera njirayi; ndipo anamuuza Abimeleki. |
| 26 |
| Ndipo Gaala, mwana wa Ebedi anadza ndi abale ake, napita ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamkhulupirira. |
| 27 |
| Ndipo anatuluka kunka kuminda, natchera mphesa m'mindamo, naponda mphesa, napereka nsembe yolemekeza, nalowa m'nyumba ya mulungu wao, nadya, namwa, natemberera Abimeleki. |
| 28 |
| Pamenepo Gaala, mwana wa Ebedi anati, Abimeleki ndani, ndi Sekemu ndani, kuti timtumikire? Sindiye mwana wa Yerubaala kodi? Ndi Zebuli kazembe wake? Mutumikire amuna a Hamori atate wa Sekemu; koma ameneyo timtumikire chifukwa ninji? |
| 29 |
| Mwenzi anthu awa akadakhala m'dzanja langa; ndikadamchotsadi Abimeleki. Ndipo anati kwa Abimeleki, Chulukitsa khamu lako, nutuluke. |
| 30 |
| Pamene Zebuli woyang'anira mudzi anamva mau a Gaala mwana wa Ebedi, anapsa mtima. |
| 31 |
| Natuma mithenga kwa Abimeleki ku Aruma monyenga nati, Taonani Gaala mwana wa Ebedi ndi abale ake afika ku Sekemu; ndipo taonani, akupandukitsirani mudzi. |
| 32 |
| Ndipo tsopano, taukani usiku, inu ndi anthu okhala nanu ndi kulalira kuthengo; |
| 33 |
| ndipo kukhale kuti m'mawa, pakutuluka dzuwa, muuke mamawa mugwere mudziwo; ndipo taonani, akakutulukirani iye ndi anthu ali naye, uzimchitira monga lidziwa dzanja lako. |
| 34 |
| Pamenepo Abimeleki anauka ndi anthu onse anali naye, usiku; nalalira a ku Sekemu, magulu anai. |
| 35 |
| Ndipo Gaala mwana wa Ebedi anatuluka, naima polowera pa chipata cha mudzi; naika Abimeleki ndi anthu anali naye m'molalira. |
| 36 |
| Ndipo pamene Gaala anapenya anthuwo anati kwa Zebuli, Taona, alikutsika anthu kuchokera pamwamba pa mapiri. Koma Zebuli ananena naye, Uona mthunzi wa mapiri ndi kuyesa anthu. |
| 37 |
| Koma Gaala ananenanso, nati, Tapenya alikutsika anthu pakati pa dziko, ndi gulu limodzi lidzera njira ya ku thundu wa alauli. |
| 38 |
| Pamenepo Zebuli anati kwa iye, Pakamwa pako mpoti tsopano, muja udanena, Ndani Abimeleki kuti timtumikire? Awa si anthuwo unawapeputsa? Utuluke tsopano, nulimbane nao. |
| 39 |
| Ndipo Gaala anatuluka pamaso pao pa eni ake a ku Sekemu, nalimbana ndi Abimeleki. |
| 40 |
| Koma Abimeleki anampirikitsa, nathawa iye pamaso pake; nagwa olasidwa ambiri mpaka polowera pa chipata. |
| 41 |
| Ndipo Abimeleki anakhala ku Aruma; ndi Zebuli anaingitsa Gaala ndi abale ake kuti asakhale m'Sekemu. |
| 42 |
| Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti anthu anatuluka kunka kuminda; ndipo anauza Abimeleki. |
| 43 |
| Pamenepo anatenga anthu, nawagawa magulu atatu, nalalira m'minda; napenya, ndipo taonani, anthu alimkutuluka m'mudzi; nawaukira iye nawakantha. |
| 44 |
| Ndi Abimeleki ndi magulu okhala naye anathamanga naima polowera pa chipata cha mudzi; ndi magulu awiriwo anagwera onse okhala m'munda, nawakantha. |
| 45 |
| Ndipo Abimeleki analimbana ndi mudzi tsiku lija lonse; nalanda mudzi nawapha anthu anali m'mwemo; napasula mudzi; nawazapo mchere. |
| 46 |
| Ndipo pamene eni ake onse a nsanja ya ku Sekemu anachimva, analowa m'ngaka ya nyumba ya Eliberiti. |
| 47 |
| Ndipo anauza Abimeleki kuti amuna onse a nsanja ya ku Sekemu asonkhane. |
| 48 |
| Pamenepo Abimeleki anakwera kunka kuphiri la Zalimoni, iye ndi anthu onse anali naye; natenga nkhwangwa m'dzanja lake Abimeleki, nadula nthambi kumitengo, nainyamula ndi kuiika paphewa pake, nati kwa anthu okhala naye, Ichi munachiona ndachita, fulumirani, muchite momwemo. |
| 49 |
| Ndi anthu onse anadulanso yense nthambi yake, natsata Abimeleki, naziika pangaka, natentha nazo ngakayo ndi moto; motero anthu onse a nsanja ya ku Sekemu anafanso, amuna ndi akazi ngati chikwi chimodzi. |
| 50 |
| Pamenepo Abimeleki anamuka ku Tebezi, naumangira Tebezi misasa, naulanda. |
| 51 |
| Koma m'mudzimo munali nsanja yolimba nathawira kumeneko amuna ndi akazi onse, ndi eni ake onse a mudziwo, nadzitsekereza m'mwemo, nakwera patsindwi pa nsanja. |
| 52 |
| Ndipo Abimeleki anafika kunsanja, nalimbana nayo nkhondo, nayandikira kukhomo kwa nsanja, aitenthe ndi moto. |
| 53 |
| Ndipo mkazi wina anaponya mwana wa mphero pamutu pa Abimeleki, naphwanya bade lake. |
| 54 |
| Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye. |
| 55 |
| Pamene amuna a Israele anaona kuti adafa Abimeleki anamuka yense kumalo kwake. |
| 56 |
| Momwemo Mulungu anambwezera Abimeleki choipacho anachitira atate wake ndi kuwapha abale ake makumi asanu ndi awiri. |
| 57 |
| Ndipo Mulungu anawabwezera choipa chonse cha amuna a ku Sekemu pamitu pao, ndipo linawagwera temberero la Yotamu mwana wa Yerubaala. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/judges/009.mp3
21
9