Davide adati, “Paja maŵa kuli phwando la mwezi wokhala chatsopano, ndipo sindiyenera kulephera kukadya ndi mfumu. Koma undilole ndipite kuti ndikabisale ku thengo mpaka mkucha madzulo.
Abambo ako akandifuna, uŵauze kuti, ‘Davide adandiwumiriza kuti ndimlole kuti athamangire ku mzinda wakwao ku Betelehemu. Akuti kumeneko kuli nsembe yapachaka ya banja lonse.’
Nchifukwa chake undikomere mtima, poti udachita chipangano ndi ine kapolo wako pamaso pa Chauta. Koma ngati ndalakwa, undiphe ndiwe osati ukanditule kwa abambo ako.”
Adakhala pa mpando wake pafupi ndi khoma, monga m'mene ankachitira nthaŵi zonse. Yonatani adakhala popenyana naye, ndipo Abinere adakhala pambali pa mfumu Saulo, koma pa malo a Davide panalibe munthu.
Koma pa tsiku lachiŵiri la phwandolo, pa malo a Davide panalibenso munthu. Ndiye Saulo adafunsa Yonatani kuti, “Chifukwa chiyani Davide mwana wa Yese sadabwere ku phwando dzulo ngakhalenso lero?”
Apo Saulo adapsera mtima Yonatani kwambiri, ndipo adamuuza kuti, “Iwe mwana wobadwa kwa chimkazi chapakamwa, kodi ukuyesa kuti sindikudziŵa ine kuti ukugwirizana ndi mwana wa Yese, amene afuna kukuchititsa manyazi iwe ndi mai wakoyo?
Tsono mnyamatayo atapita, Davide adatulukira ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, ndipo adadzigwetsa pansi nagunditsa nkhope yake pansi katatu. Adampsompsonana, nayamba kulira onse aŵiriwo, koma Davide adalira koposa.
Pamenepo Yonatani adauza Davide kuti, “Pita ndi mtendere, pakuti aŵirife tidalonjezana molumbira m'dzina la Chauta kuti, ‘Chauta ndiye adzakhale mboni pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa zidzukulu zanga ndi zidzukulu zako mpaka muyaya.’ ” Pompo Davide adanyamuka nachokapo, ndipo Yonatani adabwerera kumzinda kuja.