× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kabardian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong Tibetian South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chisunda Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Bagri Bhilali Bodo Braj Tulu Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Mazanderani Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dagbani Edo Kituba Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 BL 1992 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 2 SAMUELE GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 18 1234567891011121314151617181920212223241 1 1 : 1 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132331 1 1 Buku Lopatulika 2 SAMUELE 18 Sungani Zolemba 1Ndipo Davide anawerenga anthu amene anali naye, nawaikira atsogoleri a zikwi ndi atsogoleri a mazana.2Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang'anire Yoabu, lina aliyang'anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yoabu, ndi lina aliyang'anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzaturuka limodzi ndi inu.3Koma anthuwo anati, Simudzaturuka ndinu; pakuti tikathawa sadzatisamalira ife; ngakhale limodzi la magawo awiri a ife likafa sadzatisamalira; koma inu mulingana ndi zikwi khumi a ife; cifukwa cace tsono nkwabwino kuti mutithandize kuturuka m'mudzi.4Ndipo mfumu inanena nao, Ndidzacita cimene cikomera inu. Mfumu niima pambali pa cipata, ndipo anthu onse anaturuka ali mazana, ndi zikwi.5Ndipo mfumu inalamulira Yoabu nd Abisai ndi ltai, kuti, Cifukwa ca ine mucite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu.6Comweco anthuwo anaturukira kuthengo kukamenyana ndi Israyeli; nalimbana ku nkhalango ya ku Efraimu.7Ndipo anthu a Israyeli anakanthidwa pamenepo pamaso pa anyamata a Davide, ndipo kunali kuwapha kwakukuru kumeneko tsiku lomwelo, anthu zikwi makumi awiri.8Pakuti nkhondo inatanda pa dziko lonse, ndipo tsiku lomwelo nkhalango inaononga anthu akuposa amene anaonongeka ndi lupanga.9Ndipo Abisalomu anakomana ndi anyamata a Davide. Abisalomu naberekeka pa nyuru yace, ndipo nyuruyo inapita pansi pa nthambi zolimba za thundu wamkuru. Ndipo mutu wace unakodwa ndi mtengo, iye ali lende pakati pa thambo ndi pansi ndi nyuru imene inali pansi pa iye Inapitirira.10Ndipo munthu wina anamuona, nauza Yoabu, nati, Onani, ndaona Abisalomu ali lende pathundu.11Ndipo Yoabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? ndipo ine ndikadakupatsa ndarama khumi ndi lamba.12Munthuyo nanena ndi Yoabu, Ndingakhale ndikalandira ndarama cikwi m'dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m'kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi ltai, kuti, Cenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu.13Ndikadacita conyenga pa moyo wace, palibe mrandu ubisika kwa mfumu; ndipo inu nomwe mukadanditsuta.14Pomwepo Yoabu anati, Sindiyenera kucedwa nawe. Natenga mikondo itatu nagwaza nayo mtima wa Abisalomu alikukhala wamoyo pakati pa mtengowo.15Ndipo anyamata khumi onyamula zida zace za Yoabu anamzungulira Abisalomu namkantha namupha.16Ndipo Yoabu analiza lipenga, ndipo anthu anabwerera naleka kupitikitsa Aisrayeli; pakuti Yoahu analetsa anthuwo.17Ndipo anatenga Abisalomu namponya m'cidzenje cacikuru kunkhalangoko; naunjika pamwamba pace mulu waukuru ndithu wamiyala; ndipo Aisrayeli onse anathawa yense ku hema wace.18Koma Abisalomu akali moyo adatenga nadziutsira coimiritsaco ciri m'cigwa ca mfumu; pakuti anati, Ndiribe mwana wamwamuna adzakhala cikumbutso ca dzina langa; nacha coimiritsaco ndi dzina la iye yekha; ndipo cichedwa cikumbutso ca Abisalomu, kufikira lero lomwe.19Pomwepo Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, Ndithamange nditengere mfumu mau kuti Yehova wabwezera cilango adani ace.20Ndipo Yoabu ananena naye, Sudzakhala iwe wotengera mau lero, koma tsiku lina udzatengera mau; koma lero sudzatengera mau, cifukwa mwana wa mfumu wafa.21Pamenepo Yoabu ananena ndi Mkusi, Kauze mfumu zimene unaziona. Ndipo Mkusi anawerama kwa Yoabu, nathamanga.22Ndipo Ahimaazi mwana wa Zadoki ananena kaciwiri kwa Yoabu, Komatu, mundilole ndithamange inenso kutsata Mkusi. Ndipo Yoabu anati, Udzathamangiranji, mwana wanga, popeza sudzalandira mphotho ya pa mauwo?23Koma ngakhale kotero, anati iye, Ndithamange, iye nanena naye, Thamanga. Ndipo Ahimaazi anathamanga njira ya kucigwa, napitirira Mkusi.24Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la cipata ca kulinga, natukula maso ace, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha.25Pamenepo mlondayo anapfuula, nauza mfumu. Mfumuyo niti, Ngati ali yekha alikubwera ndi mau. Ndipo iye uja anayenda msanga, nayandikira.26Ndipo mlondayo anaona munthu wina wothamanga; mlonda naitana wakucipata nanena, Taona munthu wina wakuthamanga yekha. Ndipo mfumu inati, iyenso abwera ndi mau.27Mlondayo nati, Ndiyesa kuti kuthamanga kwa wapatsogoloyo kunga kuthamanga kwa Ahimaazi mwana wa Zadoki, Ndipo mfumu inati, iye ndiye munthu wabwino, alikubwera ndi mau okoma.28Ndipo Ahimaazi anapfuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yace pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu.29Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yoabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringu piringu, koma sindinadziwa ngati kutani.30Ndipo mfumu inati, Pambuka nuime apa. Napambuka, naimapo.31Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera cilango lero onse akuukira inu.32Ndipo mfumu inanena ndi Mkusiyo, Mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Mkusiyo nayankha, Adani a mbuye wanga mfumu, ndi onse akuukira inu kukucitirani zoipa, akhale monga mnyamata ujayo.33Ndipo mfumuyo inagwidwa cisoni, nikwera ko cipinda cosanja pa cipataco, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society Buku Lopatulika 2 SAMUELE 18 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/2samuel/018.mp3 24 18