× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 BL 1992 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 1 MAFUMU GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 1 123456789101112131415161718192021221 1 1 : 1 12345678910111213141516171819202122232425262728293031323334353637383940414243444546474849505152531 1 1 Buku Lopatulika 1 MAFUMU 1 Sungani Zolemba 1NDIPO mfumu Davide anakalamba nacuruka masiku ace; ndipo iwo anampfunda ndi zopfunda, koma iye sanafundidwa.2Pamenepo anyamata ace ananena naye, Amfunire mbuye wanga mfumu namwali, aimirire pamaso pa mfumu namsunge; nagone m'mfukato mwanu, kuti mbuye mfumu yanga afundidwe.3Tsono anafunafuna m'malire monse a Israyeli namwali wokongola, napeza Abisagi wa ku-Sunamu, nabwera naye kwa mfumu.4Ndipo namwaliyo anali wokongola ndithu, namasunga mfumu namtumikira; koma mfumu sinamdziwa.5Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agareta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga.6Ndipo atate wace sadambvuta masiku ace onse, ndi kuti, Wlitero cifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu.7Ndipo anapangana ndi Yoabu mwana wa Zeruya, ndi Abyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza.8Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wace wa Yehoyada, ndi Natani mneneri, ndi Simeyi, ndi Reyi, ndi anthu amphamvu aja adali ndi Davide, sanali ndi Adoniya.9Ndipo Adoniya anapha nkhosa ndi ng'ombe ndi nyama zonona pamwala pa Zoheleti, uli pafupi ndi citsime ca Rogeli, naitana abale ace onse ana a mfumu, ndi anthu onse a Yuda anayamata a mfumu;10koma Natani mneneriyo, ndi Benaya, ndi anthu amphamvu aja, ndi Solomo mbale wace, sanawaitana.11Pamenepo Natani ananena ndi Batiseba amace wa Solomo, nati, Kodi sunamva kuti Adoniya mwana wa Hagiti walowa ufumu, ndipo Davide mbuye wathu sadziwa?12Ubwere tsono, ndikupangire, kuti usunge moyo wako, ndi moyo wa mwana wako Solomo.13Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirira mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wadfumu? ndipo Adoniya akhaliranji mfumu?14Taona, uli cilankhulire ndi mfumu, inenso ndidzalowa pambuyo pako, ndi kutsimikiza mau ako.15Pamenepo Batiseba analowa kwa mfumu kucipinda; ndipo mfumuyo inali yokalamba ndithu; ndipo Abisagi wa ku Sunamu anali kutumikira mfumu.16Ndipo Batiseba anawerama nalambira mfumu, ndi mfumu niti, Ufunanji?17Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wacifumu.18Ndipo tsopano taonani, Adoniva walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu simudziwa.19Ndipo iye anapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi Abyatara wansembe, ndi Yoabu kazembe wa nkhondo; koma Solomo mnyamata wanu sanamuitana.20Ndipo tsopano, mbuye wanga mfumu, maso a Aisrayeli onse ali pa inu, kuti muwauze amene adzakhala pa mpando wacifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye,21Mukapanda kutero, kudzacitika, pamene mbuye wanga mfumu atagona kwa makolo ace, ine ndi mwana wanga Solomo tidzayesedwa ocimwa.22Ndipo taona, iye ali cilankhulire ndi mfumu, Natani mneneriyo analowamo.23Ndipo anauza mfumu, kuti, Wafika Natani mneneriyo. Ndipo iye anafika pamaso pa mfumu, naweramitsa nkhope yace pansi pamaso pa mfumu.24Ndipo Natani anati, Mbuye wanga mfumu, kodi inu munati, Adoniya adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala ndiye pa mpando wanga wacifumu?25Popeza iye watsika lero, nakapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pace, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya.26Koma ine, inde inedi mnyamata wanu, ndi Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Solomo mnyamata wanu, sanatiitana.27Cinthu ici cacitika ndi mbuye wanga mfumu kodi, ndipo simunadziwitsa mnyamata wanu amene adzakhala pa mpando wacifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye?28Tsono mfumu Davide anayankha, nati, Ndiitanireni Batiseba. Ndipo iye analowa pamaso pa mfumu, naima pamaso pa mfumu.29Ndipo mfumu inalumbira, niti, Pali Yehova amene anapulumutsa moyo wanga m'nsautso monse,30zedi monga umo ndinalumbirira iwe pa Yehova Mulungu wa Israyeli, ndi kuti, Zoonadi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wacifumu m'malo mwa ine, zedi nditero lero lomwe.31Pamenepo Batiseba anaweramitsa pansi nkhope yace, nalambira mfumu, nati, Mbuye wanga mfumuakhale ndi moyo nthawi zamuyaya.32Ndipo mfumu Davide anati, Kandiitanireni Zadoki wansembeyo, ndi Natani mneneriyo, ndi Benaya mwana wa Yehoyada. Iwo nalowa pamaso pa mfumu.33Ndipo mfumu inati kwa iwo, Tengani akapolo a mfumu yanu, nimukweze Solomo mwana wanga pa nyuru yanga yanga, nimutsikire naye ku Gihoni.34Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israyeli; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomo akhale ndi moyo.35Pamenepo mumtsate iye, iye nadzadza nadzakhala pa mpando wanga wacifumu, popeza adzakhala iyeyu mfumu m'malo mwanga; ndipo ndamuika iye akhale mtsogoleri wa lsrayeli ndi Yuda.36Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu.37Monga umo Yehova anakhalira ndi mbuye wanga mfumu, momwemo akhalenso ndi Solomo, nakuze mpando wace wacifumu upose mpando wacifumu wa mbuye wanga mfumu Davide.38Pamenepo Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja anatsika, nakweza Solomo pa nyuru ya mfumu Davide, nafika naye ku Gihoni.39Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali m'Cihema, namdzoza Solomo. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomo akhale ndi moyo.40Ndipo anthu onse anakwera namtsata, naliza zitoliro, nakondwera ndi kukondwera kwakukuru, kotero kuti pansi panang'ambikandiphokosolao.41Ndipo Adoniya ndi oitanidwa onse anali ndi iye analimva atatha kudya. Ndipo Yoabu, pakumva kuomba kwa lipengalo, anati, Phokosolo ndi ciani kuti m'mudzi muli cibumo?42iye akali cilankhulire, taona, walowa Yonatani mwana wa Abyatara wansembe, ndipo Adoniya anati, Lowa, popeza ndiwe munthu wamphamvu, nubwera nao uthenga wabwino.43Ndipo Yonatani anayankha, nati kwa Adoniya, Zedi Davide mbuye wathu mfumu walonga Solomo ufumu:44ndipo mfumu yatumanso Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja, namkweza iye pa nyuru ya mfumu.45Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri anamdzoza mfumu ku Gihoni, ndipo acokera kwneneko cikondwerere, ndi m'mudzimo muli phokoso. Ndilo phokoso limene mwamvali.46Ndiponso Solomo wakhala pa cimpando ca ufumu.47Ndiponso akapolo a mfumu anadzadalitsa Davide mbuye wathu mfumu, nati, Mulungu wanu aposetse dzina la Solomo lipunde dzina lanu, nakulitse mpando wace wacifumu upose mpando wanu wacifumu; ndipo mfumu anawerama pakamapo.48Ndiponso watero mfumu, Wolemekezeka Yehova Mulungu wa Israyeli, amene wapereka lero wina wokhala pa mpando wanga wacifumu, maso anga ali cipenyere.49Pamenepo oitanidwa onse a Adoniya anacita mantha, nanyamuka, napita yense njira yace.50Ndipo Adoniya anaopa cifukwa ca Solomo, nanyamuka, nakagwira nyanga za guwa la nsembe.51Ndipo anthu anakauza Solomo, kuti, Taonani, Adoniya aopa mfumu Solomo, popeza taonani, wagwira nyanga za guwa la nsembe, nati, Mfumu Solomo alumbirire ine lero kuti sadzandipha kapolo wace ndi lupanga.52Ndipo Solomo anati, iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lace limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye coipa, adzafadi.53Tsono mfumu Solomo anatuma anthu nakamtsitsa ku guwa la nsembe. Iye nadza, nagwadira mfumu Solomo; Solomo nati kwa iye, Pita kwanu.Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society Buku Lopatulika 1 MAFUMU 1 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/1kings/001.mp3 22 1