× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dagbani Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 BL 1992 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 MASALIMO GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 106 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435363738394041424344454647484950515253545556575859606162636465666768697071727374757677787980818283848586878889909192939495969798991001011021031041051061071081091101111121131141151161171181191201211221231241251261271281291301311321331341351361371381391401411421431441451461471481491501 1 1 : 1 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435363738394041424344454647481 1 1 Buku Lopatulika MASALIMO 106 Sungani Zolemba 1Haleluya. Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino: Pakuti cifundo cace ncosatha.2Adzafotokoza ndani nchito zamphamvu za Yehova, Adzamveketsa ndani cilemekezo cace conse?3Odala iwo amene asunga ciweruzo, Iye amene acita cilungamo nthawi zonse.4Mundikumbukile, Yehova, monga momwe mubvomerezana ndi anthu anu; Mundionetsa cipulumutso canu:5Kuti ndione cokomaco ca osankhika anu, Kuti ndikondwere naco cikondwerero ca anthu anu, Kuti ndidzitamandire pamodzi ndi colowa canu.6Talakwa pamodzi ndi makolo athu; Tacita mphulupulu, tacita coipa.7Makolo athu sanadziwitsa zodabwiza zanu m'Aigupto; Sanakumbukila zacifundo zanu zaunyinji; Koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.8Koma anawapulumutsa cifukwa ca dzina lace, Kuti adziwitse cimphamvu cace.9Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, niiphwa: Potero anawayendetsa mozama ngati m'cipululu.10Ndipo anawapulumutsa m'dzanja la iye amene anawada, Nawaombola ku dzanja la mdani.11Ndipo madziwo anamiza owasautsa; Sanatsala mmodzi yense.12Pamenepo anabvomereza mau ace; Anayimbira comlemekeza.13Koma anaiwala nchito zace msanga; Sanalindira uphungu wace:14Popeza analaka-lakatu kucidikhako, Nayesa Mulungu m'cipululu.15Ndipo anawapatsa copempha iwo; Koma anaondetsa mitima yao.16Ndipo kumisasa anacita nao nsanje Mose Ndi Aroni woyerayo wa Yehova.17Dziko lidayasama nilidameza Datani, Ndipo linafotsera gulu la Abiramu.18Ndipo m'gulu mwao mudayaka moto; Lawi lace lidapsereza oipawo.19Anapanga mwana wa ng'ombe ku Horebu, Nagwadira fano loyenga.20M'mwemo anasintha ulemerero wao Ndi fanizo la ng'ombe Yakudya msipu.21Anaiwala Mulungu mpulumutsi wao, Amene anacita zazikulu m'Aigupto;22Zodabwiza m'dziko la Hamu, Zoopsa ku Nyanja Yofiira.23Potero Iye adati awaononge, Pakadapanda Mose wosankhika wace, kuima pamaso pace pagamukapo, Kubweza ukali wace ungawaononge,24Anapeputsanso dziko lofunika, Osabvomereza mau ace;25Koma anadandaula m'mahema mwao, Osamvera mau a Yehova.26Potero anawasamulira dzanja lace, Kuti awagwetse m'cipululu:27Kugwetsanso mbeu zao mwa amitundu, Ndi kuwabalalitsa m'maiko maiko.28Ndipo anadzipatikiza ndi BaalaPeori, Nadyanso nsembe za akufa.29Ndipo anamkwiyitsa nazo zocita zao; Kotero kuti mliri unawagwera.30Pamenepo panauka Pinehasi, nacita cilango: Ndi mliriwo unaletseka.31Ndipo adamuyesa iye wacilungamo, Ku mibadwo mibadwo ku nthawi zonse.32Anautsanso mkwiyo wace ku madzi a Meriba, Ndipo kudaipira Mose cifukwa ca iwowa:33Pakuti anawawitsa mzimu wace, Ndipo analankhula zosayenera ndi milomo yace.34Sanaononga mitunduyo ya anthu, Imene Mulungu adawauza;35Koma anasokonekerana nao amitundu, Naphunzira nchito zao:36Ndipo anatumikira mafano ao, Amene anawakhalira msampha:37Ndipo anapereka ana ao amuna ndi akazi nsembe ya kwa ziwanda,38Nakhetsa mwazi wosacimwa, ndi wo mwazi wa ana ao amuna ndi akazi, Amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani; M'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.39Ndipo anadziipsa nazo nchito zao, Nacita cigololo nao macitidwe ao.40Potero udayaka mkwiyo wa Yehova pa anthu ace, Nanyansidwa Iye ndi colowa cace.41Ndipo anawapereka m'manja a amitundu; Ndipo odana nao anacita ufumu pa iwo.42Adani ao anawasautsanso, Nawagonjetsa agwire mwendo wao.43Iye anawalanditsa kawiri kawiri; Koma anapikisana ndi Iye mwa uphungu wao, Ndi mphulupulu zao zinawafoketsa,44Koma anapenya nsautso yao, Pakumva kupfuula kwao:45Ndipo anawakumbukila cipangano cace, Naleza monga mwa kucuruka kwa cifundo cace.46Ndipo anawacitira kuti apeze nsoni Pamaso pa onse amene adawamanga ndende.47Tipulumutseni, Yehova, Mulungu wathu, Ndi kutisokolotsa kwa amitundu, Kuti tiyamike dzina lanu loyera, Ndi kudzitamandira naco cilemekezo canu.48Wodala Yehova, Mulungu wa Israyeli, Kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndi anthu onse anene, Amen. Haleluya,Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society Buku Lopatulika MASALIMO 106 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/106.mp3 150 106