× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 BL 1992 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 MIYAMBO GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 23 123456789101112131415161718192021222324252627282930311 1 1 : 1 12345678910111213141516171819202122232425262728293031323334351 1 1 Buku Lopatulika MIYAMBO 23 Sungani Zolemba 1Pamene ukhala ulinkudya ndi mkuru, Zikumbukira ameneyo ali pamaso pako;2Nuike mpeni pakhosi pako, Ngati uli wadyera.3Usakhumbe zolongosoka zace; Pokhala zakudya zonyenga.4Usadzitopetse kuti ulemere; Leka nzeru yako yako.5Kodi upenyeranji cimene kulibe? Pakuti cuma cunera mapiko, Ngati mphungu youluka mumlengalenga.6Usadye zakudya zace za wa maso ankhwenzule, Ngakhale kukhumba zolongosoka zace;7Pakuti monga asinkha m'kati mwace, ali wotere; Ati kwa iwe, Idya numwe; Koma mtima wace suli pa iwe.8Pakuti nthongo imene unaidya udzaisanza, Ndi kutaya mau ako okondweretsa.9Usalankhule m'makutu a wopusa; Pakuti adzapeputsa nzeru ya mau ako.10Usasunthe cidziwitso cakale ca m'malire; Ngakhale kulowa m'minda ya amasiye;11Pakuti Mombolo wao walimba; Adzawanenera mlandu wao pa iwe.12Lozetsa mtima wako kumwambo, Ndi makutu ako ku mau a nzeru.13Usamane mwana cilango; Pakuti ukammenya ndi ntyole safa ai.14Udzammenya ndi ntyole, Nudzapulumutsa moyo wace kunsi kwa manda.15Mwananga, mtima wako ukakhala wanzeru, Mtima wanga wa inedi udzakondwa;16Imso zanga zidzasangalala, Polankhula milomo yako zoongoka.17Mtima wako usacitire nsanje akucimwawo; Koma opabe Yehova tsiku lonse;18Pakutitu padzakhala mphotho; Ndipo ciyembekezo cako sicidzalephereka.19Tamvera tsopano, mwananga, utenge nzeru, Ulunjikitse mtima wako m'njiramo.20Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, Ndi ankhuli osusuka.21Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; Ndipo kusinza kudzabveka munthu nsanza.22Tamvera atate wako anakubala, Usapeputse amako atakalamba.23Gula ntheradi, osaigulitsa; Nzeru, ndi mwambo, ndi luntha.24Atate wa wolungama adzasekeradi; Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.25Atate wako ndi amako akondwere, Amako wakukubala asekere.26Mwananga, undipatse mtima wako, Maso ako akondwere ndi njira zanga,27Pakuti mkazi wadama ndiye dzenje lakuya; Ndipo mkazi waciwerewere ndiye mbuna yopapatiza.28Pakuti abisalira ngati wacifwamba, Nacurukitsa anthu a ciwembu.29Ndani ali ndi cisoni? ndani asauka? ndani ali ndi makangano? Ndani ang'ung'udza? ndani alasidwa cabe? ndani afiira maso?30Ngamene acedwa pali vinyo, Napita kukafunafuna vinyo wosanganizidwa.31Usayang'ane pavinyo alikufiira. Alikung'azimira m'cikho. Namweka mosalala.32Pa citsiriziro cace aluma ngati njoka, Najompha ngati mamba.33Maso ako adzaona zacilendo, Mtima wako udzalankhula zokhota.34Udzafanana ndi wina wogona pakati pa nyanja, Pena wogona pa nsonga ya mlongoti wa ngalawa.35Udzati, Anandimenya, osaphwetekedwa ine; Anandikwapula, osamva ine; Ndidzauka nthawi yanji? Ndidzafuna-funanso vinyoyo.Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society Buku Lopatulika MIYAMBO 23 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/proverbs/023.mp3 31 23