× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 BL 1992 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 YESAYA GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 1 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435363738394041424344454647484950515253545556575859606162636465661 1 1 : 1 123456789101112131415161718192021222324252627282930311 1 1 Buku Lopatulika YESAYA 1 Sungani Zolemba 1MASOMPHENYA a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.2Imvani, miyamba inu, chera makutu, iwe dziko lapansi, cifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.3Ng'ombe idziwa mwini wace, ndi buru adziwa pomtsekereza: koma Israyeli sadziwa, anthu anga sazindikira.4Mtundu wocimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakucita zoipa, ana amene acita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israyeli, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo.5Nanga bwanji mukali cimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka.6Kucokera pansi pa phazi kufikira kumutu m'menemo mulibe cangwiro; koma mabala, ndi mikwingwirima, ndi zironda; sizinapole, ngakhale kumangidwa, ngakhale kupakidwa mafuta.7Dziko lanu liri bwinja; midzi yanu yatenthedwa ndi moto; dziko lanu alendo alimkudya pamaso panu; ndipo liri labwinja monga lagubuduzidwa ndi alendo.8Ndipo mwana wamkazi wa Ziyoni wasiyidwa ngati citando ca m'munda wamphesa, ngati cilindo ca m'munda wamankhaka, ngati mudzi wozingidwa ndi nkhondo.9Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang'onong'ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora.10Imvani mau a Yehova inu olamulira a Sodomu, cherani makutu ku cilamulo ca Mulungu wathu, inu anthu a Gomora.11Nditani nazo nsembe zanu zocurukazo? ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa ana a nkhosa, ngakhale wa atonde.12Pakudzaonekera inu pamaso pa Ine, ndani wafuna cimeneci m'dzanja lanu, kupondaponda m'mabwalo mwanga?13Musadze nazonso, nsembe zacabecabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi sabata, kumema masonkhano, sindingalole mphulupulu ndi masonkhano.14Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi za mapwando anu mtima wanga uzida; zindibvuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo.15Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pocurukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.16Sambani, dziyeretseni; cotsani macitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kucita zoipa;17phunzirani kucita zabwino; funani ciweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.18Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale ziri zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.19Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko,20koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; cifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.21Mudzi wokhulupirika wasanduka wadama! wodzala ciweruzowo! cilungamo cinakhalamo koma tsopano ambanda.22Siliva wako wasanduka mphala, vinyo wako wasanganizidwa ndi madzi.23Akuru ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera mirandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.24Cifukwa cace Yehova ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israyeli, Ha! ndidzatonthoza mtima wanga pocotsa ondibvuta, ndi kubwezera cilango adani anga;25ndipo ndidzaikanso dzanja langa pa iwe, ndi kukusungunula kukusiyanitsa iwe ndi mphala yako, ndipo ndidzacotsa seta wako wonse:26ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga paciyambi; pambuyo pace udzachedwa Mudzi wolungama, mudzi wokhulupirika.27Ziyoni adzaomboledwa ndi ciweruzo, ndi otembenuka mtima ace ndi cilungamo.28Koma kupasula kwa olakwa ndi kwa ocimwa kudzakhala kumodzi, ndi iwo amene asiya Yehova adzathedwa.29Cifukwa adzakhala ndi manyazi, cifukwa ca mitengo yathundu munaikhumba, ndipo inu mudzagwa nkhope, cifukwa ca minda imene mwaisankha.30Cifukwa mudzakhala ngati mtengo wathundu, umene tsamba lace linyala, ngatinso munda wopanda madzi.31Ndimo wamphamvu adzakhala ngati cingwe cabwazi, ndi nchito yace ngati nthethe; ndipo zonse zidzayaka moto pamodzi, opanda wozimitsa.Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society Buku Lopatulika YESAYA 1 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/isaiah/001.mp3 66 1