× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 BL 1992 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 EZEKIELE GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 1 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435363738394041424344454647481 1 1 : 1 123456789101112131415161718192021222324252627281 1 1 Buku Lopatulika EZEKIELE 1 Sungani Zolemba 1NDIPO kunali caka ca makumi atatu, mwezi wacinai, tsiku lacisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.2Tsiku lacisanu la mwezi, ndico caka cacisanu ca kutengedwa ndende mfumu Yoyakini,3anadzadi mau a Yehova kwa Ezekieli wansembe, mwana wa Buzi, m'dziko la Akasidi kumtsinje Kebara; ndi pomwepo dzanja la Yehova lidamkhalira.4Ndinapenya, ndipo taonani, mkuntho wa mphepo wocokera kumpoto, mtambo waukuru ndi moto wopfukusika m'mwemo, ndi pozungulira pace padacita ceza, ndi m'kati mwace mudaoneka ngati citsulo cakupsa m'kati mwa moto.5Ndi m'kati mwace mudaoneka mafaniziro a zamoyo zinai. Ndipo maonekedwe ao ndiwo anafanana ndi munthu,6ndi yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense wa iwo anali nao mapiko anai.7Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi ku mapazi ao kunanga kuphazi kwa mwana wa ng'ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa.8Zinali naonso manja a munthu pansi pa mapiko ao pa mbali zao zinai; ndipo zinaizi zinali nazo nkhope zao ndi mapiko ao.9Mapiko ao analumikizana; sizinatembenuka poyenda; ciri conse cinayenda ndi kulunjika kutsogoloko.10Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya ku dzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng'ombe pa mbali ya ku dzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya ciombankhanga.11Ndi nkhope zao ndi mapiko ao zinagawikana kumutu; ciri conse cinali nao mapiko awiri olumikizana, ndi awiri anaphimba thupi.12Ndipo zinayenda, ciri conse cinalunjika kutsogolo kwace uko mzimu unafuna kumukako zinamuka, sizinatembenuka poyenda.13Kunena za mafaniziro a zamoyozo, maonekedwe ao ananga makara amoto, monga maonekedwe a miyuni; motowo unayendayenda pakati pa zamoyozo, ndi motowo unacita ceza, ndi m'motomo mudaturuka mphezi.14Ndipo zamoyozo zinathamanga ndi kubwerera, ngati maonekedwe a mphezi yong'anima.15Ndipo pakupenyerera ine zamoyozo, taonani, njinga imodzi imodzi yoponda pansi pafupi ndi zamoyozo pa nkhope zao zinai.16Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana.17Poyenda zinayenda ku mbali zao zinai, zosatembenuka poyenda.18Ndi mikombero yace inali yokuzika ndi yoopsa; ndi izi zinai zinali ndi mikombero yao yodzala ndi maso pozungulira pao.19Ndipo poyenda zamoyozo, njingazi zinayenda pambali pao; ndipo ponyamuka pansi zamoyozo, njinga zinanyamuka.20Kuli konse mzimu ukuti umuke, zinamuka komwe mzimu ukuti umuke; ndi njingazi zinanyamuka pambali pa izo; pakuti mzimu wa zamoyozo unali m'njingazo.21Poyenda zija zinayenda izi, poima zija zinaima izi; ndipo ponyamuka pansi zija njingazi zinanyamuka pambali pa izo; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mu njingazi.22Ndi pa mitu ya zamoyozi panali cifaniziro ca thambo, monga mawalidwe a krustalo woopsa, loyalika pamwamba pamitu pao.23Ndi pansi pa thambolo mapiko ao analunjikana, lina kulunjika ku linzace; ciri conse cinali nao mapiko awiri akuphimba matupi ao, cakuno ndi cauko.24Ndipo pakuyenda izi ndinamva mkokomo wa mapiko ao, ngati mkokomo wa madzi akulu, ngati mau a Wamphamvuyonse, phokoso lakusokosera ngati phokoso la ankhondo; pakuima zinagwetsa mapiko ao.25Ndipo panamveka mau pamwamba pa thambolo linali pamwamba pa mitu yao; pakuima izi zinagwetsa mapiko ao.26Ndi pamwamba pa thambo linali pamitu pao panali cifaniziro ca mpando wacifumu, maonekedwe ace ngati mwala wa safiro; ndipo pa cifaniziro ca mpando wacifumu panali cifaniziro ngati maonekedwe ace a munthu wokhala pamwamba pace.27Ndipo ndinapenya ngati citsulo cakupsa, ngati maonekedwe ace a moto m'kati mwace pozungulira pace, kuyambira maonekedwe a m'cuuno mwace ndi kumwamba kwace; ndipo kuyambira maonekedwe a m'cuuno mwace ndi kunsi kwace ndinaona ngati maonekedwe ace a moto; ndi kunyezimira kudamzinga.28Ngati maonekedwe a utawaleza uli m'mtambo tsiku la mvula, momwemo maonekedwe a kunyezimira kwace pozungulira pace. Ndiwo maonekedwe a cifaniziro ca ulemerero wa Yehova. Ndipo pakucipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mau a wina wakunena.Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society Buku Lopatulika EZEKIELE 1 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/ezekiel/001.mp3 48 1