× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 BL 1992 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 OBADIYA GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 1 11 1 1 : 1 1234567891011121314151617181920211 1 1 OBADIYA 1 Sungani Zolemba 1MASOMPHENYA a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yocokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo.2Taona, ndakuika wamng'ono mwa amitundu; unyozedwa kwambiri.3Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwace, Adzanditsitsira pansi ndani?4Cinkana ukwera pamwamba peni peni ngati ciombankhanga, cinkana cisanja cako cisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova.5Akakudzera akuba, kapena mbala usiku, (Ha! waonongeka) sadzaba mpaka adzakhuta kodi? Akakudzera akuchera mphesa sadzasiya khunkha kodi?6Ha! za Esau zasanthulidwa; ha! zobisika zace zafunidwa.7Anthu onse a akupangana nawe anakuperekeza mpaka pamalire; anthu okhala ndi mtendere nawe anakunyenga, nakuposa mphamvu; iwo akudya cakudya cako akuchera msampha pansi pako; mulibe nzeru mwa iye.8Ati Yehova, Kodi sindidzaononga tsiku lija anzeru mwa Edomu, ndi luntha m'phiri la Esau?9Ndipo amuna anu amphamvu adzatenga nkhawa, Temani iwe, kuti onse aonongeke m'phiri la Edomu, ndi kuphedwa.10Cifukwa ca ciwawa unamcitira mphwako Yakobo, udzakutidwa ndi manyazi, nudzaonongeka ku nthawi yonse.11Tsiku lija unaima padera, tsiku lija alendo anagwira ndende makamu ace, nalowa m'zipata zace acilendo, nacitira Yerusalemu maere, iwenso unakhala ngati mmodzi wa iwowa.12Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka cikhakha tsiku lakupsinjika.13Usalowe m'mudzi wa anthu anga tsiku la tsoka lao, kapena kupenyerera iwe coipa cao tsiku la tsoka lao, kapena kuthira manja khamu lao tsiku la tsoka lao.14Ndipo usaime pamphambano kuononga opulumuka ace; kapena kupereka otsala ace tsiku lakupsinjika.15Pakuti tsiku la Yehova layandikira amitundu onse; monga unacita iwe, momwemo adzakucitira; cocita iwe cidzakubwererapamtupako.16Pakuti monga munamwa pa phiri langa lopatulika, momwemo amitundu onse adzamwa kosalekeza; inde adzamwa, nadzameza, nadzakhala monga ngati sanalipo.17Koma m'phiri la Ziyoni mudzakhala opulumuka, ndipo lidzakhala lopatulika; ndi a nyumba ya Yakobo adzakhala nazo zolowa zao.18Ndipo nyumba ya Yakobo idzakhala moto, ndi nyumba ya Yosefe lawi, ndi nyumba ya Esau ngati ciputu, ndipo adzawatentha pakati pao, ndi kuwapsereza; ndipo sadzakhalapo otsalira nyumba ya Esau; pakuti Yehova wanena.19Ndipo akumwela adzakhala nalo phiri la Esau colowa cao; ndi iwo a kucidikha adzakhala nalo dziko la Afilisti; ndipo adzakhala nayo minda ya Efraimu, ndi minda ya Samariya colowa cao; ndi Benjamini adzakhala nalo la Gileadi.20Ndipo andende a khamu ili la ana a Israyeli, okhala mwa Akanani, adzakhala naco colowa cao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala m'Sefaradi adzakhala nayo midzi ya kumwela, colowa cao.21Ndipo apulumutsi adzakwera pa phiri la Ziyoni kuweruza phiri la Esau; ndipo ufumu udzakhala wace wa Yehova.Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society Buku Lopatulika OBADIYA 1 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/obadiah/001.mp3 1 1