× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 BL 1992 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 NUMERI GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 1 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435361 1 1 : 1 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435363738394041424344454647484950515253541 1 1 Buku Lopatulika NUMERI 1 Sungani Zolemba 1NDIPO Yehova ananena ndi Mose m'cipululu ca Sinai, m'cihema cokomanako, tsiku loyamba la mwezi waciwiri, caka caciwiri ataturuka m'dziko la Aigupto, ndi kuti,2Werenga khamu lonse la ana a Israyeli, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba ya makolo ao ndi kuwerenga maina ao, amuna onse mmodzi mmodzi.3Iwe ndi Aroni muwawerenge monga mwa magulu ao, onse m'Israyeli akuturuka kunkhondo, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu,4Ndipo pamodzi ndi inu pakhale munthu mmodzi wa mapfuko onse; yense mkuru wa nyumba ya kholo lace.5Ndipo maina a amuna amene aime nanu ndi awa: wa Rubeni, Elizuri mwana wa Sedeuri.6Wa Simeoni, Selumiyeli mwana wa Zurisadai.7Wa Yuda, Nahesoni mwana wa Aminadabu.8Wa Isakara, Netaneli mwana wa Zuwara.9Wa Zebuloni, Eliyabu mwana wa Heloni.10Wa ana a Yosefe: wa Efraimu, Elisama mwana wa Amihudi; wa Manase, Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.11Wa Benjamini, Abidana mwana wa Gideoni.12Wa Dani, Ahiyezeri mwana wa Amisadai.13Wa Aseri, Pagiyeli mwana wa Okirani.14Wa Gadi, Eliyasafe mwana wa Deyueli.15Wa Nafitali, Ahira mwana wa Enani.16Iwo ndiwo oitanidwa a khamu, akalonga a mapfuko a makolo ao; ndiwo akuru a zikwizo za Israyeli.17Ndipo Mose ndi Aroni anatenga anthu awa, onenedwa maina ao;18nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi waciwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kuchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzi mmodzi.19Monga Yehova anauza Mose, momwemo anawawerenga m'cipululu ca Sinai.20Ndipo ana a Rubeni, mwana woyamba wa Israyeli, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina mmodzi mmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;21owerengedwa ao a pfuko la Rubeni, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi cimodzi kudza mazana asanu.22A ana a Simeoni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, owerengedwa ao, powerenga maina mmodzi mmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;23owerengedwa ao a pfuko la Simeoni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu.24A ana a Gadi, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;25owerengedwa ao a pfuko la Gadi, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu.26A ana a Yuda, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makomi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;27owerengedwa ao a pfuko la Yuda, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.28A ana a Isakara, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;29owerengedwa ao a pfuko la lsakara, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai.30A ana a Zebuloni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;31owerengedwa ao a pfuko la Zebuloni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai.32A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efraimu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;33owerengedwa ao a pfuko la Efraimu, ndiwo zikwi makumi anai mphambu mazana asanu.34A ana a Manase, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;35owerengedwa ao a pfuko la Manase, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri.36A ana a Benjamini, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;37owerengedwa ao a pfuko la Benjamini, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai.38A ana a Dani, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;39owerengedwa ao a pfuko la Dani, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.40A ana a Aseri, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;41owerengedwa ao a pfuko la Aseri, ndiwo zikwi makumi anai mphambu cimodzi kudza mazana asanu.42A ana a Nafitali, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;43owerengedwa ao a pfuko la Nafitali, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.44Iwo ndiwo amene anawerengedwa, amene Mose anawerenga pamodzi ndi Aroni, ndi akalonga a Israyeli, ndiwo amuna khumi ndi awiri; yense kunenera nyumba ya kholo lace.45Potero owerengedwa onse a ana a Israyeli monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo m'Israyeli;46inde owerengedwa onse ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.47Koma Alevi monga mwa pfuko la makolo ao sanawerengedwa mwa iwo.48Popeza Yehova adalankhula ndi Mose, ndi kuti,49Pfuko la Levi lokha usaliwerenge, kapena kuona kufikira kwao mwa ana a Israyeli;50koma iwe, uike Alevi asunge kacisi wa mboni, ndi zipangizo zace zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula kacisi, ndi zipangizo zace zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa kacisi.51Ndipo akati amuke naye kacisiyo, Aleviamgwetse, ndipo akati ammange, Alevi amuimike; ndipo mlendo akayandikizako amuphe,52Ndipo ana a Israyeli amange mahema ao, yense ku cigono cace, ndi yense ku mbendera yace, monga mwa makamu ao.53Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa kacisi wa mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israyeli; ndipo Alevi azidikira kacisi wa mboni.54Momwemo ana a Israyeli anacita monga mwa zonse Yehova adauza Mosel anacita momwemo.Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society Buku Lopatulika NUMERI 1 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/numbers/001.mp3 36 1