× Chilankhulo Europe Chirasha Chibelarusi Chiyukireniya Chipolishi Chiserbia Chibugariya Chislovakia Czech Chiromani Chi Moldova Azerbaijan Chiameniya Chijojiya Chialubaniya Avar Bashkir Chitata Chechen Chisiloveniya Chiroatia ChiEstonia Chilativiya Chilithuania Chihangare Chifinishi Chinorway Chiswedwe Chi Icelandic Chi Greek Chimakedoniya Chijeremani Bavarian Chidatchi Chidanishi Chiwelsh Chi Gaelic Chiairishi Chifalansa Basque Chikatalani Chitaliyana Chitchainizi Achiroma Bosnian Kumpoto kwa Amerika Chingerezi South America Chisipanishi Chipwitikizi Chiguarani Quechuan Aymara Central America Chaku Jamaican Chilankhulo Chichewa Qeqchi Chaku Haiti Kum'mawa kwa Asia Chitchaina Chijapani Korea Chimongoliya Uyghur Hmong South East Asia Chimalaysian Chibama Chin Chinepali Cebuano Chitagalogi Wachikambodiya Chi Thai Chiindoneziya Chivietinamu Chijava Lao Iban IuMien Kachin Lahu Aceh Balinese Bugis Pampanga Sasak Shan Waray Kumwera kwa Asia Chihindi Оdia Awadhi Mizo Chikannada Malayalam Kambikatha Chimarathi Chigujarati Tamil Chilankhulo Chipunjabi Kurukh Assamese Maithili Chibengali Chiurdu Sinhala Dogri Haryanvi Meitei Konkani Santali Sindhi Koya Thado Sanskrit Devanagari Adilabad Gondi Ahirani Balochi Bundeli Chhattisgarhi Garhwali Kangri Kumaoni Mewari Munda Sadri Seraiki Shekhawati Sylheti Central Asia Chikigizi Chiuzbeki Chitajik Anthu aku Turkmen Kazakhstan Karakalpak Kuulaya Chituruki Chihebri Chiarabu Persian Chikurdi Chiashto Chikoputiki Africa Chiafrikaana Chixhosa Chizulu Ndebele Sotho Chiamhariki Wolaytta Waku Nigeria Mossi Ika Dinka Kabyle Ewe Chiswahili Morocco Wachisomali Chishona Madagascar Chiigbo Lingala Baoule Chiswati Chitsonga Chitswana Gambia Chiyoruba Kamba Chikinyarwanda Chihausa Chewa Chiluo Makua Dyula Fulfulde Kalenjin Kikuyu Kikwango Kirundi Krio Nigerian Pidgin Oromo Tshiluba Tshivenda Twi Umbundu Lugbara Luguru Pular Gussi Maasai Turkana Moba Nuer Shilluk Tamasheq Makonde Bemba Fon Hadiyya Ibibio Kimbundu Kimiiru Lango Liberian Kreyol Lomwe Mende Morisyen Ndau Nyankole Sena Sidamo Soga Songe Sukuma Tarifit Teso Tiv Zande Dziko la Australia New Zealand Papua New Guinea Ziyankhulo Zakale Chiaramu Chilatini Chiesperanto 1 1 1 BL 1992 2016Buku Lopatulika 2014BL 1992BLYDC1 1 1 MARKO GENESISEKSODOLEVITIKONUMERIDEUTERONOMOYOSWAOWERUZARUTE1 SAMUELE2 SAMUELE1 MAFUMU2 MAFUMU1 MBIRI2 MBIRIEZARANEHEMIYAESTEREYOBUMASALIMOMIYAMBOMLALIKINYIMBO YA SOLOMONIYESAYAYEREMIYAMALIROEZEKIELEDANIELEHOSEYAYOWELEAMOSIOBADIYAYONAMIKANAHUMUHABAKUKUZEFANIYAHAGAIZEKARIYAMALAKI--- --- ---MATEYUMARKOLUKAYOHANEMACHITIDWE A ATUMWIAROMA1 AKORINTO2 AKORINTOAGALATIYAAEFESOAFILIPIAKOLOSE1 ATESALONIKA2 ATESALONIKA1 TIMOTEO2 TIMOTEOTITOFILEMONIAHEBRIYAKOBO1 PETRO2 PETRO1 YOHANE2 YOHANE3 YOHANEYUDACHIVUMBULUTSO1 1 1 1 123456789101112131415161 1 1 : 1 1234567891011121314151617181920212223242526272829303132333435363738394041424344451 1 1 Buku Lopatulika MARKO 1 Sungani Zolemba 1CIYAMBI cace ca Uthenga Wabwino wa Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu.2Monga mwalembedwa m'Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, Amene adzakonza njira yanu;3Mau a wopfuula m'cipululu, Konzani khwalala la Ambuye, Lungamitsani njira zace;4Yohane anadza nabatiza m'cipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku cikhululukiro ca macimo.5Ndipo anaturuka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordano, poulula macimo ao.6Ndipo Yohane anabvala ubweya wa ngamila, ndi lamba lacikopa m'cuuno mwace, nadya dzombe ndi uci wa kuthengo.7Ndipo analalikira, kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula lamba la nsapato zace ine.8Ndakubatizani inu ndi madzi; koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.9Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kucokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane m'Yordano.10Ndipo pomwepo, alimkukwera poturuka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda:11ndipo mau anaturuka m'thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.12Ndipo pomwepo Mzimu anamkangamiza kunka kucipululu.13Ndipo anakhala m'cipululu masiku makumi anai woyesedwa ndi Satana; nakhala ndi zirombo, ndipo angelo anamtumikira.14Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira uthenga wabwino wa Mulungu,15nanena, Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani uthenga wabwino.16Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andreya, mbale wace wa Simoni, alinkuponya psasa m'nyanja; pakuti anali asodzi.17Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu.18Ndipo pomwepo anasiya makoka ao, namtsata Iye.19Ndipo atapita patsogolo pang'ono, anaona Yakobo, mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace, iwonso anali m'combo nakonza makoka ao.20Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedayo m'combomo pamodzi ndi anchito olembedwa, namtsata.21Ndipo iwo analowa m'Kapemao; ndipo pomwepo pa dzuwa la Sabata iye analowa m'sunagoge naphunzitsa,22Ndipo anazizwa ndi ciphunzitso cace; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi.23Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anapfuula iye24kuti, Tiri ndi ciani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife? Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.25Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli cete, nuturuke mwa iye.26Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kupfuula ndi mau akuru, unaturuka mwa iye.27Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ici nciani? ciphunzitso catsopano! ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye.28Ndipo mbiri yace inabuka pompaja ku dziko lonse la Galileya lozungulirapo.29Ndipo pomwepo, poturuka m'sunagoge, iwo analowa m'nyumba ya Simoni ndi Andreya pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane,30Ndipo mpongozi wace wa Simoni anali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo anamuuza za iye:31ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo.32Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, ndi akugwidwa ndi ziwanda.33Ndipo mudzi wonse unasonkhana pakhomo.34Ndipo anaciritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundu mitundu, naturutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalola ziwandazo zilankhule, cifukwa zinamdziwa Iye.35Ndipo m'mawa mwace anauka usikusiku, naturuka namuka kucipululu, napemphera kumeneko.36Ndipo Simoni ndi anzace anali naye anamtsata,37nampeza, nanena naye, Akufunani inu anthu onse.38Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, ku midzi iri pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera nchito imene.39Ndipo analowa m'masunagoge mwao m'Galileya monse, nalalikira, naturutsa ziwanda.40Ndipo anadza kwa Iye wodwala khate, nampempha Iye, namgwadira, ndi kunena ndi Iye, Ngati mufuna mukhoza kundikonza.41Ndipo Yesu anagwidwa cifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.42Ndipo pomwepo khate linamcoka, ndipo anakonzedwa.43Ndipo anamuuzitsa, namturutsa pomwepo,44nanena naye, Ona, usati unene kanthu kwa munthu ali yense: koma muka, ukadzionetse kwa wansembe, nupereke pa makonzedwe ako 1 zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo.45Koma 2 iye anaturuka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanadziwa kulowansopoyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a ku malo onse.Chewa Bible (BL) 1992 Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society Buku Lopatulika MARKO 1 00:00:00 00:00:00 0.5x 2.0x https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/mark/001.mp3 16 1